Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Zimene Baibulo Limaphunzitsa

Baibulo limatithandiza kupeza mayankho a mafunso ovuta kwambiri amene tingafunse pa moyo wathu. Ndipo kwa zaka zambirimbiri, mfundo zimene zili m’Baibulo zakhala zikuthandiza anthu kwambiri. M’chigawo chino, mupeza mfundo zotsimikizira kuti Baibulo ndi lothandizadi.—2 Timoteyo 3:16, 17.

Nkhani Zina Zimene Zilipo

Kodi Tingadziwe Bwanji Kuti Baibulo Limanena Zoona?

Ngati Baibulo linachokeradi kwa Mulungu, ndiye kuti liyenera kukhala losiyana kwambiri ndi mabuku ena onse.

Kodi Baibulo Limanena Kuti Kumwa Mowa Ndi Tchimo?

Baibulo limasonyeza kuti mowa ukhoza kuthandiza munthu amene akudwala m’mimba komanso likhoza kuthandiza munthu kuti azisangalala.

Zothandiza Mabanja

MABANJA

Mungatani Kuti Muzigwirizana Ndi Apongozi Anu?

Mfundo zitatu zomwe zingakuthandizeni kuti nkhani zokhudza apongozi zisasokoneze banja lanu.

MAKOLO

Kukambirana ndi Mwana Wanu Nkhani Yotumizirana Zinthu Zolaula Pafoni

Musachite kudikira kuti mpaka mwana wanu akumane ndi vuto linalake chifukwa chakuti sanagwiritse ntchito bwino foni yake. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene mungachite kuti mukambirane ndi mwana wanu kuopsa kotumizirana zinthu zolaula.

ANA

Muzimvetsera Tikakhala Pamisonkhano

N’chifukwa chiyani tiyenera kumvetsera tikakhala pamisonkhano?

MABANJA

Muzidalira Kwambiri Mulungu

Kudzifunsa mafunso awiri okha kungathandize kuti banja lanu liziyenda bwino.