Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

panitan/stock.adobe.com

NTCHITO YOITANIRA ANTHU KU CHIKUMBUTSO

Yesu Adzathetsa Umphawi

Yesu Adzathetsa Umphawi

 Ali padzikoli, Yesu anasonyeza chikondi chachikulu kwa anthu, makamaka ovutika komanso amene anali ndi nkhawa. (Mateyu 9:36) Iye anafika popereka moyo wake kuti athandize anthuwo. (Mateyu 20:28; Yohane 15:13) Posachedwapa, adzasonyeza umboni winanso wakuti amakonda anthu onse pogwiritsa ntchito mphamvu zake monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ndipo adzathetsa umphawi padziko lonse lapansi.

 Baibulo limafotokoza mwandakatulo zimene Yesu adzachite kuti:

  •   “Ateteze anthu onyozeka pakati pa anthu, Apulumutse ana a anthu osauka.”—Salimo 72:4.

 Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira zonse zimene Yesu anatichitira komanso zimene adzatichitire posachedwapa? Pa Luka 22:19, Yesu anauza otsatira ake kuti azikumbukira imfa yake. N’chifukwa chake, chaka chilichonse a Mboni za Yehova amakumana pamodzi kuti achite mwambo wokumbukira imfa yake pa tsiku limene anaphedwa. Tikukuitanani kuti mudzakhale nafe Pamwambo Wokumbukira imfa yake Lamlungu pa 24 March 2024.

Fufuzani Komwe Kudzachitikire Chikumbutso