Salimo 72:1-20

 • Ulamuliro wamtendere wa mfumu ya Mulungu

  • “Wolungama zinthu zidzamuyendera bwino” (7)

  • Adzakhala ndi anthu omugonjera kuchokera kunyanja kukafika kunyanja (8)

  • Adzawapulumutsa kuti asachitiridwe zachiwawa (14)

  • Padziko lapansi padzakhala tirigu wochuluka (16)

  • Dzina la Mulungu lidzatamandidwa mpaka kalekale (19)

Salimo lonena za Solomo. 72  Inu Mulungu, thandizani mfumu kuti iziweruza mogwirizana ndi zigamulo zanu,Ndipo dziwitsani mwana wa mfumu za chilungamo chanu.+   Ateteze anthu anu pa mlandu wawo pogwiritsa ntchito chilungamo,Aweruze mwachilungamo milandu ya anthu anu onyozeka.+   Mapiri abweretse mtendere kwa anthu,Ndipo zitunda zibweretse chilungamo.   Ateteze* anthu onyozeka pakati pa anthu,Apulumutse ana a anthu osauka,Ndipo aphwanye wobera anzake mwachinyengo.+   Iwo adzakuopani kwa nthawi yonse imene dzuwa lidzakhalepoKomanso kwa nthawi yonse imene mwezi udzakhalepo,Adzakuopani ku mibadwomibadwo.+   Adzakhala ngati mvula imene imagwera pa udzu umene watchetchedwa,Ngati mvula yamvumbi imene imanyowetsa nthaka.+   Mʼmasiku a ulamuliro wake, wolungama zinthu zidzamuyendera bwino,*+Ndipo padzakhala mtendere wochuluka+ kwa nthawi yonse imene mwezi udzakhalepo.   Iye adzakhala ndi anthu omugonjera* kuchokera kunyanja kukafika kunyanja,Komanso kuchokera ku Mtsinje* kukafika kumalekezero a dziko lapansi.+   Anthu amene amakhala mʼchipululu adzamugwadira,Ndipo adani ake adzabwira fumbi.+ 10  Mafumu a ku Tarisi komanso amʼzilumba adzapereka msonkho.+ Mafumu a ku Sheba ndi ku Seba adzapereka mphatso.+ 11  Mafumu onse adzamugwadira,Ndipo mitundu yonse ya anthu idzamutumikira. 12  Chifukwa adzapulumutsa wosauka amene akufuula popempha thandizo,Komanso wonyozeka ndi aliyense amene alibe womuthandiza. 13  Adzamvera chisoni munthu wonyozeka ndi wosauka,Ndipo adzapulumutsa miyoyo ya anthu osauka. 14  Adzawapulumutsa* kuti asaponderezedwe komanso kuchitiridwa zachiwawa,Ndipo adzaona kuti magazi awo ndi amtengo wapatali. 15  Iye akhale ndi moyo wautali ndipo apatsidwe golide wa ku Sheba.+ Nthawi zonse anthu azimupempherera,Ndipo azimudalitsa tsiku lililonse. 16  Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri.+Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka. Zokolola za mfumu zidzachuluka ngati mitengo ya ku Lebanoni,+Ndipo mʼmizinda, anthu adzaphuka ngati udzu wapanthaka.+ 17  Dzina lake likhalebe mpaka kalekale,+Ndipo lipitirize kutchuka kwa nthawi zonse pamene dzuwa lidzakhalepo. Ndipo kudzera mwa iye, anthu apeze madalitso.+Mitundu yonse ya anthu imutchule kuti ndi wosangalala. 18  Atamandike Yehova Mulungu, Mulungu wa Isiraeli,+Iye yekha amene amachita zinthu zodabwitsa.+ 19  Litamandike dzina lake laulemerero mpaka kalekale,+Ndipo ulemerero wake udzaze dziko lonse lapansi.+ Ame! Ame! 20  Mapemphero a Davide mwana wa Jese, athera pamenepa.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Aweruze.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wolungama adzaphuka.”
Kapena kuti, “Iye adzalamulira.”
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Kapena kuti, “Adzawombola miyoyo yawo.”