Salimo 139:1-24

  • Mulungu amadziwa bwino atumiki ake

    • Palibe amene angathawe mzimu wa Mulungu (7)

    • “Munandipanga modabwitsa” (14)

    • “Maso anu anandiona ngakhale pamene ndinali mluza” (16)

    • “Munditsogolere mʼnjira yamuyaya” (24)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la Davide. 139  Inu Yehova, mwandifufuza ndipo mukundidziwa.+  2  Inu mumadziwa ndikakhala pansi komanso ndikaimirira.+ Mumadziwa maganizo anga muli kutali.+  3  Mumandiona* ndikamayenda komanso ndikagona.Mumadziwa chilichonse chimene ndikuchita.+  4  Ndisananene kanthu,Inu Yehova mumakhala mutadziwa kale zonse.+  5  Mwandizungulira mbali zonse,Ndipo mwaika dzanja lanu pa ine.  6  Kwa ine nʼzovuta kwambiri kuti ndimvetse zinthu zimenezi.* Ndi zapamwamba kwambiri moti sindingathe kuzifikira.+  7  Kodi ndingapite kuti kuthawa mzimu wanu,Ndipo ndingapite kuti kuthawa nkhope yanu?+  8  Ngati ndingakwere kumwamba, inu mudzakhala komweko,Ndipo ngati ndingayale bedi langa ku Manda,* taonani! inunso mudzakhala komweko.+  9  Ngati ndingauluke pamapiko amʼbandakuchaKuti ndikakhale mʼnyanja yakutali kwambiri, 10  Ngakhale kumenekonso dzanja lanu lidzanditsogoleraNdipo dzanja lanu lamanja lidzandigwira.+ 11  Ngati ndinganene kuti: “Ndithudi mdima undibisa!” Pamenepo mdima umene wandizungulira udzasanduka kuwala. 12  Ngakhale mdimawo sudzakhala mdima wandiweyani kwa inu,Koma usiku udzawala ngati masana.+Mdima udzangokhala ngati kuwala kwa inu.+ 13  Inu munapanga impso zanga.Munanditeteza* ndili mʼmimba mwa mayi anga.+ 14  Ndimakutamandani chifukwa munandipanga modabwitsa+ ndipo zimenezi zimandichititsa mantha. Ntchito zanu ndi zodabwitsa,+Ine ndikudziwa bwino zimenezi. 15  Mafupa anga sanali obisika kwa inuPa nthawi imene ndinkapangidwa kumalo amene aliyense sakanatha kuona,Pamene munkandiwomba ngati nsalu mʼmalo apansi kwambiri padziko lapansi.+ 16  Maso anu anandiona ngakhale pamene ndinali mluza.*Ziwalo zanga zonse zinalembedwa mʼbuku lanuMʼbukumo munalembedwa za masiku amene zinapangidwa,Zinalembedwa chiwalo chilichonse chisanapangidwe. 17  Choncho kwa ine maganizo anu ndi ofunika kwambiri, inu Mulungu,+ Ndipo ndi ochuluka kwambiri.+ 18  Nditati ndiyese kuwawerenga, angakhale ochuluka kwambiri kuposa mchenga.+ Podzuka ndingakhale ndikuwawerengabe.*+ 19  Inu Mulungu, zikanakhala bwino mukanapha oipa.+ Zikanatero anthu achiwawa* akanachoka kwa ine, 20  Anthu amene amanena zinthu zokhudza inu ndi zolinga zoipa.*Amenewa ndi adani anu amene amagwiritsa ntchito dzina lanu molakwika.+ 21  Inu Yehova, pajatu ine ndimadana ndi anthu amene amadana nanu,+Ndipo ndimanyansidwa ndi anthu amene amakupandukirani.+ 22  Ndimadana nawo kwambiri.+Kwa ine akhala adani enieni. 23  Ndifufuzeni inu Mulungu, ndipo mudziwe mtima wanga.+ Ndifufuzeni ndipo mudziwe maganizo anga amene akundidetsa nkhawa.*+ 24  Muone ngati mwa ine muli chilichonse choipa,+Ndipo munditsogolere+ mʼnjira yamuyaya.

Mawu a M'munsi

^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Mumandiyeza.”
^ Kapena kuti, “Zinthu zimenezi ndi zodabwitsa kwambiri kwa ine.”
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Mabaibulo ena amati, “Munandiwumba pamodzi.”
^ “Mluza” ndi mwana amene wangoyamba kumene kupangidwa mʼmimba mwa mayi ake.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ndimakhala ndidakali ndi inu.”
^ Kapena kuti, “amene ali ndi mlandu wa magazi.”
^ Kapena kuti, “Anthu amene amanena zamʼmutu mwawo zokhudza inu.”
^ Kapena kuti, “amene akundisowetsa mtendere.”