Salimo 28:1-9
-
Mulungu anayankha pemphero la amene analemba salimo
-
‘Yehova ndi mphamvu yanga komanso chishango changa’ (7)
-
Salimo la Davide.
28 Ndikuitana inu Yehova, Thanthwe langa,+Musatseke makutu anu pamene ine ndikuitana.
Mukakhala chete pamene ndikukuitanani,Ndidzafanana ndi anthu amene akutsikira kudzenje la manda.+
2 Imvani mawu anga ochonderera pamene ndikufuulira inu kuti mundithandize,Pamene ndikukweza manja anga, nditayangʼana kumene kuli chipinda chamkati chamʼmalo anu opatulika.+
3 Musandikokolole pamodzi ndi anthu oipa, amene amachita zopweteka anzawo,+Anthu amene amalankhula mawu amtendere ndi anzawo, koma mʼmitima yawo muli zinthu zoipa.+
4 Muwabwezere mogwirizana ndi zochita zawo,+Mogwirizana ndi zochita zawo zoipa.
Abwezereni mogwirizana ndi ntchito za manja awo,Mogwirizana ndi zimene achita.+
5 Chifukwa iwo sachita chidwi ndi zochita za Yehova,+Kapena ntchito za manja ake.+
Mulungu adzawagwetsa ndipo sadzawamanga.
6 Atamandike Yehova,Chifukwa iye wamva kuchonderera kwanga kopempha thandizo.
7 Yehova ndi mphamvu yanga+ komanso chishango changa.+Mtima wanga umamukhulupirira.+
Iye wandithandiza, moti mtima wanga ukusangalala.Choncho ndidzamutamanda ndi nyimbo yanga.
8 Yehova ndi mphamvu kwa anthu ake,Iye ndi malo achitetezo, amapereka chipulumutso chachikulu kwa wodzozedwa wake.+
9 Pulumutsani anthu anu, ndipo dalitsani cholowa chanu.+
Mukhale mʼbusa wawo ndipo muwanyamule mʼmanja mwanu mpaka kalekale.+