Salimo 32:1-11

  • Osangalala ndi anthu amene machimo awo akhululukidwa

    • “Ndinaulula tchimo langa kwa inu” (5)

    • Mulungu amakupatsani nzeru (8)

Salimo la Davide. Masikili.* 32  Wosangalala ndi munthu amene zolakwa zake zakhululukidwa, amene machimo ake akhululukidwa.+   Wosangalala ndi munthu amene Yehova sakumuona kuti ndi wolakwa,+Amene alibe mtima wachinyengo.   Pamene ndinakhala chete osaulula machimo anga, mafupa anga anafooka, chifukwa ndinkavutika mumtima mwanga tsiku lonse.+   Dzanja lanu linkandilemera* masana ndi usiku.+ Mphamvu zanga zinauma* ngati madzi mʼnyengo yotentha yachilimwe. (Selah)   Pamapeto pake ndinaulula tchimo langa kwa inu,Sindinabise cholakwa changa.+ Ndinati: “Ndidzaulula machimo anga kwa Yehova.”+ Ndipo inu munandikhululukira zolakwa zanga ndi machimo anga.+ (Selah)   Nʼchifukwa chake aliyense wokhulupirika adzapemphera kwa inu+Mwayi wokuyandikirani udakalipo.+ Akatero ngakhale madzi osefukira sadzamupeza.   Ndinu malo anga obisalamo,Mudzanditeteza ku mavuto.+ Mwachititsa kuti ndizunguliridwe ndi anthu amene akufuula mosangalala chifukwa chakuti mwandipulumutsa.+ (Selah)   Inu munati: “Ndidzakupatsa nzeru komanso kukulangiza njira yoti uyendemo.+ Ndidzakupatsa malangizo ndi kukuyangʼanira.+   Anthu inu, musakhale ngati hatchi kapena nyulu* yosazindikira,+Imene munthu amachita kuimanga chingwe pakamwa pake kuti athetse kupulupudza kwake,Akatero mʼpamene imatha kumuyandikira.” 10  Zopweteka za woipa ndi zambiri.Koma wokhulupirira Yehova amatetezedwa ndi chikondi Chake chokhulupirika.+ 11  Inu olungama, kondwerani chifukwa cha zimene Yehova wachita ndipo sangalalani.Fuulani mosangalala inu nonse owongoka mtima.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Mkwiyo wanu unkandilemera”
Kapena kuti, “Chinyontho cha moyo wanga chinasintha.”
“Nyulu” ndi nyama yooneka ngati hatchi.