Salimo 116:1-19

  • Nyimbo yoyamikira

    • “Yehova ndidzamubwezera chiyani?” (12)

    • “Ndidzamwa zamʼkapu yachipulumutso” (13)

    • “Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova” (14, 18)

    • Imfa ya anthu okhulupirika ndi yopweteka kwambiri (15)

116  Ndimakonda YehovaChifukwa amamva mawu anga komanso kuchonderera kwanga kopempha thandizo.+   Amatchera khutu lake nʼkundimvetsera,*+Ndipo ndidzaitanira pa iye moyo wanga wonse.*   Zingwe za imfa zinandikulunga.Ndinkangomva ngati ndatsala pangʼono kufa.+ Ndinavutika chifukwa cha nkhawa komanso chisoni.+   Koma ndinaitana pa dzina la Yehova kuti:+ “Inu Yehova, ndipulumutseni!”   Yehova ndi wokoma mtima* komanso wolungama.+Mulungu wathu ndi wachifundo.+   Yehova amateteza anthu osadziwa zambiri.+ Ndinafooka chifukwa cha nkhawa koma iye anandipulumutsa.   Moyo wanga upumulenso,Chifukwa Yehova wandichitira zinthu mokoma mtima.   Inu mwandipulumutsa ku imfa,Mwapukuta misozi yanga ndipo mwateteza phazi langa kuti lisapunthwe.+   Ndidzayenda pamaso pa Yehova mʼdziko la anthu amoyo. 10  Ndinali ndi chikhulupiriro, nʼchifukwa chake ndinalankhula.+Ndinavutika kwambiri. 11  Nditapanikizika ndinati: “Munthu aliyense ndi wabodza.”+ 12  Yehova ndidzamubwezera chiyaniPa zabwino zonse zimene wandichitira? 13  Ndidzamwa zamʼkapu yachipulumutso,*Ndipo ndidzaitana pa dzina la Yehova. 14  Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova,Pamaso pa anthu ake onse.+ 15  Mʼmaso mwa YehovaImfa ya anthu ake okhulupirika ndi yopweteka kwambiri.*+ 16  Ndikukupemphani, inu Yehova,Chifukwa ine ndi mtumiki wanu. Ndine mtumiki wanu, mwana wa kapolo wanu wamkazi. Mwamasula zingwe zimene anandimanga nazo.+ 17  Ndidzapereka nsembe zoyamikira kwa inu,+Ndipo ndidzaitana pa dzina la Yehova. 18  Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova,+Pamaso pa anthu ake onse,+ 19  Mʼmabwalo a nyumba ya Yehova,+Pakati pa iwe Yerusalemu. Tamandani Ya!*+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “amawerama kuti andimvetsere.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmasiku anga.”
Kapena kuti, “ndi wachisomo.”
Kapena kuti, “yachipulumutso chachikulu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi nkhani yaikulu.”
Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.