Salimo 85:1-13
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+
85 Inu Yehova, dziko lanu mwalisonyeza kukoma mtima.+Mwabwezeretsa ana a Yakobo amene anagwidwa ukapolo.+
2 Munakhululukira anthu anu zolakwa zawo.Munawakhululukira* machimo awo onse.+ (Selah)
3 Munabweza mkwiyo wanu wonse,Ndipo simunasonyeze mkwiyo wanu waukulu.+
4 Tibwezeretseni mwakale,* inu Mulungu amene mumatipulumutsa,Ndipo tichotsereni mkwiyo wanu.+
5 Kodi mutikwiyira mpaka kalekale?+
Kodi mudzapitiriza kusonyeza mkwiyo wanu ku mibadwomibadwo?
6 Kodi simutipatsanso mphamvuKuti anthu anu asangalale chifukwa cha inu?+
7 Tisonyezeni chikondi chanu chokhulupirika inu Yehova,+Ndipo mutipulumutse.
8 Ndidzamvetsera zimene Mulungu woona Yehova adzanene,Chifukwa adzanena za mtendere kwa anthu ake,+ kwa okhulupirika ake.Koma iwo asayambenso kudzidalira kwambiri ngati kale.+
9 Ndithudi, iye ndi wokonzeka kupulumutsa amene amamuopa,+Kuti ulemerero wake ukhale mʼdziko lathu.
10 Chikondi chokhulupirika komanso kukhulupirika zidzakumana.Chilungamo ndi mtendere zidzakisana.+
11 Kukhulupirika kudzaphuka padziko lapansi,Ndipo chilungamo chidzayangʼana pansi kuchokera kumwamba.+
12 Ndithudi, Yehova adzapereka zinthu zabwino,*+Ndipo dziko lathu lidzapereka zokolola zake.+
13 Chilungamo chidzayenda pamaso pake,+Ndipo chidzapanga njira kuti mapazi a Mulungu azidutsamo.
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Munaphimba.”
^ Kapena kuti, “Tisonkhanitseni ndi kutibwezeretsa mwakale.”
^ Kapena kuti, “adzachititsa kuti zinthu ziziyenda bwino.”