Salimo 22:1-31
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira “Mbawala Yaikazi ya Mʼbandakucha.”* Nyimbo ya Davide.
22 Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?+
Nʼchifukwa chiyani mukuchedwa kundipulumutsa?Nʼchifukwa chiyani simukumva kubuula kwanga?+
2 Inu Mulungu wanga, ine ndimakuitanani masana, koma simundiyankha.+Ndipo usiku sindikhala chete, ndimaitanabe.
3 Koma inu ndinu woyera,+Ndipo mwazunguliridwa ndi* mawu otamanda a Isiraeli.
4 Makolo athu ankadalira inu.+Iwo ankakudalirani ndipo inu munkawapulumutsa.+
5 Iwo ankafuulira inu ndipo munkawapulumutsa.Ankakudalirani ndipo simunawakhumudwitse.*+
6 Koma ine ndine nyongolotsi osati munthu,Anthu amandinyogodola* komanso kundinyoza.+
7 Anthu onse amene amandiona amandiseka.+Iwo amandinyogodola nʼkumapukusa mitu yawo mondinyoza nʼkumati:+
8 “Anadzipereka kwa Yehova. Tiyeni tione ngati angamupulumutse!
Musiyeni Mulungu amupulumutse, chifukwa amamukonda kwambiri!”+
9 Inu ndi amene munanditulutsa mʼmimba,+Ndinu amene munandichititsa kumva kuti ndine wotetezeka pamene ndinkayamwa mabere a mayi anga.
10 Ndinaperekedwa kwa inu kuti muzindisamalira* kuyambira pamene ndinabadwa.Kuyambira ndili mʼmimba mwa mayi anga, inu mwakhala Mulungu wanga.
11 Musakhale kutali ndi ine, chifukwa mavuto ali pafupi+Ndipo palibe winanso amene angandithandize.+
12 Ngʼombe zazingʼono zamphongo zochuluka zandizungulira.+Ngʼombe zamphongo zamphamvu za ku Basana zandizungulira.+
13 Iwo atsegula pakamwa pawo nʼkumandiopseza,+Ngati mkango wobangula umene umakhadzulakhadzula nyama.+
14 Ndathiridwa pansi ngati madzi.Mafupa anga onse aguluka.
Mtima wanga wakhala ngati phula,+Ukusungunuka mkati mwanga.+
15 Mphamvu zanga zauma ngati phale.+Lilime langa lamatirira kunkhama zanga,+Ndipo mwandilowetsa mʼdzenje kuti ndife.+
16 Adani anga andizungulira ngati agalu.+Andizungulira ngati gulu la anthu ochita zoipa,+Mofanana ndi mkango, iwo akundiluma manja ndi mapazi.+
17 Ndingathe kuwerenga mafupa anga onse.+
Adaniwo akuona zimenezi ndipo akundiyangʼanitsitsa.
18 Iwo akugawana zovala zanga,Ndipo akuchita maere pa zovala zanga.+
19 Koma inu Yehova, musakhale kutali ndi ine.+
Inu ndinu mphamvu zanga, ndithandizeni mofulumira.+
20 Ndipulumutseni ku lupanga,Pulumutsani moyo wanga wamtengo wapatali* mʼkamwa* mwa agalu.+
21 Ndipulumutseni mʼkamwa mwa mkango+ komanso kunyanga za ngʼombe zamphongo zamʼtchire.Mundiyankhe ndi kundipulumutsa.
22 Ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga.+Ndidzakutamandani pakati pa mpingo.+
23 Inu amene mumaopa Yehova, mutamandeni!
Inu nonse mbadwa* za Yakobo, mʼpatseni ulemerero!+
Muopeni, inu nonse mbadwa* za Isiraeli.
24 Chifukwa iye sananyoze kapena kunyansidwa ndi kuvutika kwa munthu woponderezedwa.+Sanabise nkhope yake kwa iye.+
Pamene anamulirira kuti amuthandize, iye anamva.+
25 Ndidzakutamandani mumpingo waukulu.+Ndidzakwaniritsa malonjezo anga pamaso pa anthu amene amamuopa.
26 Ofatsa adzadya nʼkukhuta.+Anthu amene akufunafuna Yehova adzamutamanda.+
Musangalale ndi moyo* mpaka kalekale.
27 Anthu onse ochokera kumalekezero a dziko lapansi adzakumbukira Yehova nʼkupita kwa iye.
Ndipo mabanja onse a mitundu ya anthu adzagwada pamaso panu.+
28 Chifukwa Yehova ndi Mfumu,+Ndipo akulamulira mitundu ya anthu.
29 Anthu onse olemera* padziko lapansi adzadya ndipo adzamuweramira.Anthu onse amene amabwerera kufumbi adzagwada pamaso pake,Ndipo palibe aliyense wa iwo amene angapulumutse moyo wawo.
30 Mbadwa* zawo zidzamutumikira.Mibadwo yamʼtsogolo idzauzidwa zokhudza Yehova.
31 Adzabwera nʼkunena za chilungamo chake.
Adzauza anthu amene adzabadwe zimene iye wachita.
Mawu a M'munsi
^ Nʼkutheka kuti chimenechi chinali chuni kapena mtundu wa kaimbidwe.
^ Kapena kuti, “mpando wanu wachifumu uli pakati pa.”
^ Kapena kuti, “simunawachititse manyazi.”
^ Kapena kuti, “amandichitira zachipongwe.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Anandiponyera kwa inu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “wokhawu umene ndili nawo,” kutanthauza moyo wake.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmanja.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Mtima wanu ukhale ndi moyo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “onenepa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”