Salimo 24:1-10

  • Mfumu yaulemerero yalowa mʼmageti

    • ‘Dziko lapansi ndi la Yehova’ (1)

Salimo la Davide. Nyimbo. 24  Dziko lapansi ndiponso zonse zimene zili mmenemo ndi za Yehova,+Nthaka komanso onse okhala panthakapo ndi ake.   Iye anakhazika dziko lapansi molimba panyanja+Ndipo analikhazikitsa mwamphamvu pamitsinje.   Ndi ndani angakwere kuphiri la Yehova,+Ndipo ndi ndani angaime mʼmalo ake opatulika?   Aliyense amene ndi wosalakwa komanso wopanda chinyengo mumtima mwake,+Amene sanalumbire mwachinyengo potchula moyo Wanga,*Kapena kulumbira pofuna kupusitsa anthu ena.+   Iye adzalandira madalitso kuchokera kwa Yehova,+Komanso chilungamo kuchokera kwa Mulungu amene amamupulumutsa.+   Umenewu ndi mʼbadwo wa anthu amene amafunafuna Mulungu,Mʼbadwo wa anthu amene amafunafuna nkhope yanu, inu Mulungu wa Yakobo. (Selah)   Tukulani mitu yanu, inu mageti,+Tsegukani,* inu makomo akale,Kuti Mfumu yaulemerero ilowe!+   Kodi Mfumu yaulemerero imeneyi ndi ndani? Ndi Yehova, wanyonga ndi wamphamvu,+Yehova, wamphamvu pankhondo.+   Tukulani mitu yanu, inu mageti,+Tsegukani, inu makomo akale,Kuti Mfumu yaulemerero ilowe! 10  Kodi Mfumu yaulemerero imeneyi ndi ndani? Ndi Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. Iye ndi Mfumu yaulemerero.+ (Selah)

Mawu a M'munsi

Akunena za moyo wa Yehova umene munthu waulumbirira.
Kapena kuti, “Imirirani.”