Salimo 64:1-10
-
Nditetezeni ku ziwembu zobisika
-
“Mulungu adzawalasa” (7)
-
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.
64 Inu Mulungu, imvani mawu anga pamene ndikukuchondererani.+
Tetezani moyo wanga ku zinthu zoopsa zimene mdani akuchita.
2 Ndibiseni ku ziwembu zachinsinsi za anthu oipa,+Kwa gulu la anthu ochita zoipa.
3 Iwo amanola lilime lawo ngati lupanga.Amakonzekera kuponya mawu awo opweteka ngati mivi,
4 Kuti alase munthu wosalakwa atamubisalira.Amamulasa modzidzimutsa ndiponso mopanda mantha.
5 Amaumirira kuti akwaniritse zolinga zawo zoipa,*Amakambirana zimene angachite kuti abise misampha yawo.
Iwo amanena kuti: “Angaione ndani?”+
6 Amafufuza njira zatsopano zochitira zinthu zoipa.Mwachinsinsi amakonza njira zochitira ziwembu zawo mochenjera.+Zimene munthu aliyense akuganiza mumtima mwake, nʼzovuta kuzimvetsa.
7 Koma Mulungu adzawalasa ndi muvi.+Adzavulazidwa ndi muvi modzidzimutsa.
8 Adzawonongedwa chifukwa cha zolankhula za lilime lawo lomwe,+Onse amene adzaone zimenezi adzapukusa mitu yawo.
9 Ndiyeno anthu onse adzachita mantha,Ndipo adzalengeza zimene Mulungu wachita,Iwo adzamvetsa bwino zimene iye amachita.+
10 Wolungama adzasangalala chifukwa cha Yehova ndipo adzathawira kwa iye.+Onse owongoka mtima adzasangalala kwambiri.*
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Amalimbikitsana kuti achite zoipa.”
^ Kapena kuti, “adzadzitamandira.”