Salimo 132:1-18

  • Anasankha Davide komanso Ziyoni

    • “Musakane wodzozedwa wanu” (10)

    • Ansembe a ku Ziyoni adzawaveka chipulumutso (16)

Nyimbo Yokwerera Kumzinda. 132  Inu Yehova, kumbukirani DavideKomanso mavuto onse amene anakumana nawo.+  2  Kumbukirani kuti analumbira kwa inu Yehova,Analonjeza kwa Wamphamvu wa Yakobo kuti:+  3  “Sindidzalowa mutenti yanga, mʼnyumba yanga.+ Sindidzagona pabedi langa.  4  Sindidzalola kuti ndigoneKapena kutseka maso anga,  5  Mpaka nditamupezera Yehova malo okhala,Malo abwino oti* Wamphamvu wa Yakobo azikhalamo.”+  6  Ku Efurata,+ tinamva zimene zinachitika.Tinalipeza kunkhalango.*+  7  Tiyeni tilowe mʼmalo ake okhala.*+Tiyeni tiwerame pachopondapo mapazi ake.+  8  Nyamukani, inu Yehova, kuti mulowe mʼmalo anu okhalamo,+Inu pamodzi ndi Likasa limene likuimira mphamvu zanu.+  9  Ansembe anu avale chilungamo,Ndipo okhulupirika anu afuule mosangalala. 10  Chifukwa cha zimene munalonjeza Davide mtumiki wanu,Musakane* wodzozedwa wanu.+ 11  Yehova walumbira kwa Davide.Ndithudi sadzalephera kukwaniritsa mawu ake akuti: “Ndidzaika pampando wako wachifumuMmodzi wa ana ako.*+ 12  Ana ako akadzasunga pangano langaKomanso malamulo* anga amene ndikuwaphunzitsa,+Ana awonsoAdzakhala pampando wako wachifumu kwamuyaya.”+ 13  Chifukwa Yehova wasankha Ziyoni.+Akufunitsitsa kuti akhale malo ake okhalamo. Iye akuti:+ 14  “Awa ndi malo anga okhalamo mpaka kalekale.Ndidzakhala mmenemu,+ chifukwa zimenezi ndi zimene ndikulakalaka. 15  Ndidzadalitsa kwambiri malo amenewa ndi chakudya.Anthu ake osauka ndidzawapatsa chakudya chokwanira.+ 16  Ansembe ake ndidzawaveka chipulumutso,+Ndipo okhulupirika ake adzafuula mosangalala.+ 17  Kumeneko ndidzachulukitsa mphamvu* za Davide. Wodzozedwa wanga ndamukonzera nyale.+ 18  Adani ake ndidzawaveka manyazi,Koma ufumu wake udzakhala wamphamvu.”*+

Mawu a M'munsi

^ Kapena kuti, “Chihema chachikulu choti.”
^ Nʼkutheka kuti akunena zokhudza Likasa.
^ Kapena kuti, “tilowe mʼchihema chake chachikulu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Musabweze nkhope ya.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Chipatso cha mimba yako.”
^ Kapena kuti, “zikumbutso.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “nyanga.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “chisoti chake chachifumu chidzakhala champhamvu.”