Salimo 81:1-16
Kwa wotsogolera nyimbo, pa Gititi.* Salimo la Asafu.+
81 Fuulani mosangalala kwa Mulungu amene ndi mphamvu yathu.+
Fuulirani Mulungu wa Yakobo mosangalala chifukwa wapambana.
2 Yambani kuimba nyimbo ndipo tengani maseche,Zeze womveka mosangalatsa pamodzi ndi choimbira cha zingwe.
3 Pa tsiku limene mwezi watsopano waoneka,+ imbani lipenga la nyanga ya nkhosa,Pa tsiku limene mwezi wathunthu waoneka, imbani lipenga la nyanga ya nkhosa, limene limaimbidwa pa tsiku la chikondwerero.+
4 Chifukwa limeneli ndi lamulo kwa Isiraeli,Komanso chigamulo cha Mulungu wa Yakobo.+
5 Mulungu anaika chigamulocho kuti chikhale chikumbutso kwa Yosefe+Pamene ankapita kukapereka chilango mʼdziko la Iguputo.+
Ndinamva mawu amene sindinathe kuwazindikira akuti:*
6 “Ndinachotsa katundu wolemera paphewa lake.+Manja ake anamasuka moti sankanyamulanso dengu.
7 Pamene unkakumana ndi mavuto unaitana, ndipo ine ndinakupulumutsa.+Ndinakuyankha ndi mabingu ochokera mumtambo.*+
Ndinakuyesa pamadzi a ku Meriba.*+ (Selah)
8 Imvani anthu anga, ndipo ine ndipereka umboni wokutsutsani.
Inu Aisiraeli, zikanakhala bwino ngati mukanandimvera.+
9 Pakati panu sipadzakhala mulungu wachilendo,Ndipo simudzagwadira mulungu wachilendo.+
10 Ine Yehova, ndine Mulungu wanu,Amene ndinakutulutsani mʼdziko la Iguputo.+
Tsegulani kwambiri pakamwa panu ndipo ndidzaikamo chakudya.+
11 Koma anthu anga sanamvere mawu anga,Isiraeli sanafune kundigonjera.+
12 Choncho ndinawasiya kuti apitirize kuchita zofuna za mtima wawo wosamverawo.Iwo anachita zimene ankaganiza kuti nʼzoyenera.*+
13 Zikanakhala bwino ngati anthu anga akanandimvera,+Zikanakhala bwino ngati Isiraeli akanayenda mʼnjira zanga.+
14 Ndikanagonjetsa adani awo mofulumira,Ndikanalanga adani awo ndi dzanja langa.+
15 Amene amadana ndi Yehova adzachita mantha pamaso pake,Ndipo zimene zidzawachitikire* zidzakhalapo mpaka kalekale.
16 Koma iye adzakudyetsani tirigu wabwino kwambiri,*+Ndipo adzakupatsani uchi wochokera pathanthwe kuti mudye nʼkukhuta.”+
Mawu a M'munsi
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “chilankhulo chimene sindinathe kuchizindikira kuti.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmalo obisika a mabingu.”
^ Kutanthauza, “Kukangana.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Anayenda mʼmalangizo awo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “nthawi.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “adzakudyetsani mafuta a tirigu.”