Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

A3

Zimene Zinachitika Kuti Baibulo Lisungike Mpaka Pano

Amene analemba Baibulo komanso Mwiniwake ndi amene amaliteteza. Ndi amene anachititsa kuti mawu otsatirawa alembedwe:

“Mawu a Mulungu wathu adzakhala mpaka kalekale.” —Yesaya 40:8.

Zimenezi ndi zoona ngakhale kuti panopa kulibe mipukutu yoyambirira ya Baibulo ya Malemba a Chiheberi ndi Chiaramu a kapena Chigiriki. Ndiye tingatsimikize bwanji kuti zimene zili mʼBaibulo nʼzofanana ndi zimene zinali mʼmipukutu youziridwa yoyambirirayo?

OKOPERA MALEMBA ANATETEZA MAWU A MULUNGU

Chimene chinathandiza kuti Malemba a Chiheberi atetezeke ndi zimene Mulungu analamula Aisiraeli zoti azikopera Malemba. b Mwachitsanzo, Yehova analamula mafumu a Isiraeli kuti azikopera mabuku awoawo a Chilamulo. (Deuteronomo 17:18) Komanso Mulungu anapatsa Alevi udindo wosunga komanso kuphunzitsa anthu Chilamulo. (Deuteronomo 31:26; Nehemiya 8:7) Ayuda atatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo, panakhazikitsidwa gulu la anthu okopera Malemba kapena kuti alembi (Soferimu). (Ezara 7:6, mawu amʼmunsi) Patapita nthawi, alembi amenewa analemba makope ambiri a mabuku 39 a Malemba a Chiheberi.

Kwa zaka zambiri, alembiwa anakhala akukopera malemba mosamala kwambiri. Mʼzaka za mʼma 500 mpaka 1500, gulu la alembi a Chiyuda amene ankadziwika kuti Amasorete anapitiriza ntchito imeneyi. Mpukutu wakale kwambiri umene Amasorete anakopera ndi wa Leningrad Codex ndipo anamaliza kuulemba cha mʼma 1008/1009 C.E. Koma pakati pa zaka za mʼma 1900, anapeza mipukutu ina ya Baibulo kapena zidutswa zake pafupifupi 220. Mipukutu imeneyi anaipeza pamodzi ndi Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa. Mipukutu imeneyi inalembedwa zaka zoposa 1,000, mpukutu wa Leningrad Codex usanalembedwe. Tikayerekezera Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa ndi mpukutu wa Leningrad Codex timapeza mfundo yofunika kwambiri yakuti: Nʼzoona kuti pena ndi pena Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa inagwiritsa ntchito mawu osiyana ndi amene ali mu Leningrad Codex koma zimenezi sizisokoneza uthenga wake.

Nanga bwanji mabuku 27 a Malemba a Chigiriki? Mabuku amenewa analembedwa ndi ena mwa atumwi a Yesu Khristu komanso Akhristu ena oyambirira. Potengera zimene alembi a Chiyuda ankachita, Akhristu oyambirira anakopera mabukuwa. (Akolose 4:16) Ngakhale kuti Diocletian amene anali mfumu ya Roma komanso anthu ena anayesetsa kuti awononge mabuku onse amene Akhristu oyambirira anali nawo, mipukutu komanso zidutswa zambiri zakale zasungidwabe mpaka pano.

Mabuku a Chikhristu amenewa anamasuliridwanso mʼzilankhulo zina. Mabaibulo oyambirira amene anamasuliridwa mʼzilankhulo zakale anali a Chiameniya, Chikoputiki, Chiitiopiya, Chijojiya, Chilatini komanso Chisiriya.

KUSANKHA MALEMBA A CHIHEBERI KOMANSO A CHIGIRIKI OTI AMASULILIDWE

Sikuti amene analemba komanso kukopera mipukutu yakale ya Baibulo anagwiritsa ntchito mawu ofanana. Ndiye tingadziwe bwanji mawu amene anali mʼmipukutu yoyambirirayo?

Zimenezi tingaziyerekezere ndi mphunzitsi amene wauza ophunzira 100 kuti akopere chaputala chimodzi cha buku. Ngakhale chaputala choyambiriracho chitasowa, munthu angadziwe mawu amene anali muchaputala choyambiriracho akayerekezera makope 100 amene alipowo. Ngakhale kuti wophunzira aliyense angalakwitse zinthu zina, nʼzosatheka kuti ophunzira onse alakwitse zinthu zofanana. Mofanana ndi zimenezi, akatswiri akayerekezera zidutswa zambirimbiri ndi makope akale a mabuku a mʼBaibulo, amathabe kuzindikira pamene okopera analakwitsa komanso mawu oyambirira amene amayenera kugwiritsidwa ntchito.

“Tinganene motsimikiza kuti palibe buku lina lakale lomwe linakoperedwa molondola kwambiri ngati mipukutu ya Malemba a Chiheberi”

Kodi tingatsimikize bwanji kuti mfundo zimene zinali mʼmipukutu yoyambirira zinamasuliridwa molondola mʼBaibulo lathu? Ponena za Malemba a Chiheberi, katswiri wina dzina lake William H. Green analemba kuti: “Tinganene motsimikiza kuti palibe buku lina lakale lomwe linakoperedwa molondola kwambiri ngati mipukutu ya Malemba a Chiheberi.” Pofotokoza za Malemba a Chigiriki, amene amadziwikanso kuti Chipangano Chatsopano, katswiri wina wa Baibulo dzina lake F. F. Bruce anati: “Pali umboni wochuluka wakuti mabuku a Chipangano Chatsopano anamasuliridwa molondola kwambiri kuposa mabuku wamba. Komabe anthu sakayikira nʼkomwe zomwe zili mʼmabuku wambawo.” Iye anapitiriza kuti: “Zikanakhala kuti Chipangano Chatsopano ndi mabuku wamba, si bwenzi anthu akukayikira kuti mabuku ake anamasuliridwa molondola.”

Chaputala 40 cha Buku la Yesaya kuchokera mʼMipukutu ya ku Nyanja Yakufa (mipukutuyi inalembedwa kuyambira mu 125 mpaka 100 B.C.E.)

Tikayerekezera ndi mipukutu ya Chiheberi imene inapezeka patapita zaka 1,000, zimene zikusiyana, ndi zinthu zingʼonozingʼono makamaka kalembedwe ka mawu

Chaputala 40 cha Buku la Yesaya kuchokera mu Aleppo Codex, womwe ndi mpukutu wofunika wa Chiheberi wa Amasorete umene unalembedwa cha mʼma 930 C.E.

Malemba a Chiheberi: Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba a Chiheberi (1953-1960) linamasuliridwa kuchokera ku Baibulo lotchedwa Biblia Hebraica, limene linalembedwa ndi Rudolf Kittel. Kuchokera nthawi imeneyo, mʼMalemba ena a Chiheberi okonzedwanso monga Biblia Hebraica Stuttgartensia ndi Biblia Hebraica Quinta, awonjezeramo mfundo zina zimene azipeza posachedwapa kuchokera mʼMipukutu ya ku Nyanja Yakufa komanso mʼmipukutu ina yakale. Mawu amene ali mʼmabuku amenewa akufanana ndi amene ali mu Leningrad Codex ndipo anaikamonso mawu amʼmunsi amene akusonyeza mawu omwe anagwiritsidwa ntchito mʼmabuku kapena mʼmipukutu ina ngati Pentatuke wa Chisamariya, Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa, Baibulo la Chigiriki la Septuagint, ma Targum a Chiaramu, Baibulo la Chilatini la Vulgate ndi Baibulo la Chisiriya la Peshitta. Pamene Baibulo la Dziko Latsopano linkakonzedwanso, anaona zimene zili mu Biblia Hebraica Stuttgartensia komanso mu Biblia Hebraica Quinta.

Malemba a Chigiriki: Chakumapeto kwa zaka za mʼma 1800, akatswiri a Baibulo omwe ndi B. F. Westcott komanso F.J.A. Hort, anayerekezera mipukutu ya Baibulo komanso zidutswa zimene zinalipo pa nthawiyo. Iwo anachita zimenezi pamene ankalemba Malemba a Chigiriki omwe ankaona kuti ndi ofanana kwambiri ndi malemba oyambirira. Chapakati pa zaka za mʼma 1900, Komiti Yomasulira Baibulo la Dziko Latsopano inagwiritsa ntchito zimene akatswiri awiriwa analemba pomasulira Baibulo la Dziko Latsopano. Anagwiritsanso ntchito mipukutu yopangidwa ndi gumbwa yomwe akuganiza kuti ndi ya zaka za mʼma 100 ndi 200 C.E. Kungochokera nthawi imeneyo, pakhala pakupezeka mipukutu yambiri yagumbwa. Kuwonjezera pamenepo, Malemba ena ngati amene analembedwa ndi Nestle ndi Aland komanso a United Bible Societies, amasonyeza zimene akatswiri a Baibulo apeza posachedwapa. Zina zimene anapeza pofufuzapo, zagwiritsidwa ntchito mʼBaibuloli.

Tikatengera zimene zili mʼmabuku amenewo, nʼzoonekeratu kuti mavesi ena a mʼMalemba a Chigiriki amene ali mʼMabaibulo akale monga King James Version, anachita kuwonjezeredwa ndi anthu ena amene ankakopera malemba ndipo sanali mbali ya Malemba ouziridwa. Koma popeza kuti kugawa mavesi amene akugwiritsidwa ntchito mʼMabaibulo ambiri kunachitika mʼzaka za mʼma 1500, kuchotsa mavesi amenewa panopa kwachititsa kuti Mabaibulo ambiri akhale opanda mavesi mʼmalo ena. Mavesi ake ndi Mateyu 17:21; 18:11; 23:14; Maliko 7:16; 9:44, 46; 11:26; 15:28; Luka 17:36; 23:17; Yohane 5:4; Machitidwe 8:37; 15:34; 24:7; 28:29 komanso Aroma 16:24. MʼBaibuloli pamavesi amene anachotsedwawo taikapo mawu amʼmunsi.

Nʼzodziwikiratu kuti mavesi amene ali mʼmawu omaliza aatali opezeka pa Maliko 16 (vesi 9-20), mawu omaliza aafupi muchaputala 16 cha Maliko komanso mawu amene ali pa Yohane 7:53–8:11 mʼmipukutu yoyambirira munalibemo. Choncho mʼBaibuloli sitinaikemo mawu amene anawonjezeredwawo. c

Mawu ena asinthidwa kuti agwirizane ndi zimene akatswiri a Baibulo akuona kuti zikugwirizana ndi zimene zili mʼmipukutu yoyambirira. Mwachitsanzo, mogwirizana ndi zimene mipukutu ina imanena, lemba la Mateyu 7:13 limati: “Lowani pageti lalingʼono. Chifukwa msewu umene ukupita kuchiwonongeko ndi wotakasuka komanso geti lake ndi lalikulu.” Koma mu Baibulo la Dziko Latsopano lakale munalibe mawu akuti “geti lake.” Koma titafufuza mʼmipukutu tinapeza umboni wakuti mawu oti “geti lake” analipo mʼmipukutu yoyambirira. Choncho mawuwa anaikidwa mʼBaibuloli. Pali zinthu zambiri zofanana ndi zimenezi zomwe zakonzedwa. Koma zimene zasinthazi ndi zinthu zingʼonozingʼono ndipo sizikusintha uthenga wopezeka mʼMawu a Mulungu.

Mpukutu wagumbwa wa 2 Akorinto 4:13–5:4 umene unalembedwa cha mʼma 200 C.E.

a Munkhani ino tizingowatchula kuti Malemba a Chiheberi.

b Chifukwa chimodzi chimene chinachititsa kuti azikopera malemba chinali chakuti mipukutu yoyambirirayo inapangidwa ndi zinthu zomwe zikanatha kuwonongeka.

c Kuti muone chifukwa chake tikunena kuti malemba amenewa anachita kuwawonjezeramo, onani mawu amʼmunsi mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika la Malifalensi, limene linatuluka mu 1984.