Salimo 52:1-9

  • Kukhulupirira chikondi cha Mulungu chokhulupirika

    • Chenjezo kwa anthu odzitama chifukwa chochita zoipa (1-5)

    • Anthu osaopa Mulungu amadalira chuma chawo (7)

Kwa wotsogolera nyimbo. Masikili.* Salimo la Davide, pa nthawi imene Doegi wa ku Edomu, anapita kwa Sauli nʼkukamuuza kuti Davide wapita kunyumba ya Ahimeleki.+ 52  Nʼchifukwa chiyani ukudzitukumula chifukwa cha zinthu zoipa zimene ukuchita, wamphamvu iwe?+ Chikondi chokhulupirika cha Mulungu nʼchokhalitsa.+  2  Lilime lako limene ndi lakuthwa ngati lezala,+Limakonza chiwembu komanso kuchita zachinyengo.+  3  Umakonda kwambiri zinthu zoipa kuposa zabwino,Umakonda kwambiri kunama kuposa kulankhula zoona. (Selah)  4  Umakonda mawu onse opweteka ena,Iwe amene lilime lako limalankhula zachinyengo.  5  Nʼchifukwa chake Mulungu adzakugwetsa ndipo sudzakhalakonso.+Adzakugwira nʼkukukokera kutali ndi tenti yako,+Ndipo adzakuzula nʼkukuchotsa mʼdziko la anthu amoyo.+ (Selah)  6  Olungama adzaona zimenezi nʼkuchita mantha,+Ndipo adzamuseka+ kuti:  7  “Taonani, munthu uyu sanadalire Mulungu monga malo ake othawirako,*+Koma ankadalira chuma chake chochuluka,+Komanso ziwembu zimene ankapanga.”*  8  Koma ine ndidzakhala ngati mtengo waukulu wa maolivi wa masamba obiriwira mʼnyumba ya Mulungu.Ndidzadalira chikondi chokhulupirika cha Mulungu+ mpaka kalekale.  9  Ndidzakutamandani mpaka kalekale, chifukwa cha zimene mwachita.+Pamaso pa okhulupirika anu,Ndidzayembekezera dzina lanu,+ chifukwa ndi labwino.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “achitetezo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mavuto amene ankayambitsa.”