Salimo 16:1-11
Mikitamu* ya Davide.
16 Nditetezeni, inu Mulungu, chifukwa ndathawira kwa inu.+
2 Ndauza Yehova kuti: “Inu ndinu Yehova. Zinthu zonse zabwino pa moyo wanga zimachokera kwa inu.*
3 Ndipo oyera amene ali padziko lapansi,Anthu aulemerero amenewo, ndi amene amandichititsa kukhala wosangalala kwambiri.”+
4 Anthu amene amafunitsitsa kulambira milungu ina amachulukitsa chisoni chawo.+
Ine sindidzapereka nsembe zachakumwa za magazi kwa milungu ina,Ndipo milomo yanga sidzatchula mayina awo.+
5 Yehova ndi gawo langa, gawo limene ndinapatsidwa+ komanso kapu yanga.+
Inu mumateteza cholowa changa.
6 Malo amene andiyezera ndi abwino kwambiri.
Inde, ndikukhutira ndi cholowa chimene ndapatsidwa.+
7 Ndidzatamanda Yehova amene wandipatsa malangizo.+
Ngakhale usiku maganizo amkati mwa mtima wanga* amandiuza zoyenera kuchita.+
8 Ndimaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse.+
Chifukwa iye ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.*+
9 Choncho mtima wanga ukusangalala, ndikusangalala kwambiri.*
Ndipo ndikukhala motetezeka.
10 Chifukwa simudzandisiya* mʼManda.*+
Simudzalola kuti wokhulupirika wanu aone dzenje.*+
11 Mumandidziwitsa njira ya moyo.+
Ndikakhala nanu pafupi,* ndimasangalala kwambiri.+Kudzanja lanu lamanja kuli chimwemwe* mpaka kalekale.
Mawu a M'munsi
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “Ubwino wanga umachokera kwa inu.”
^ Kapena kuti, “mmene ndikumvera mumtima mwanga.” Mʼchilankhulo choyambirira, “impso zanga.”
^ Kapena kuti, “sindidzadzandira.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ulemerero wanga ukusangalala.”
^ Kapena kuti, “simudzasiya moyo wanga.”
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Mabaibulo ena amati, “avunde.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndikakhala pafupi ndi nkhope yanu.”
^ Kapena kuti, “chisangalalo.”

