Salimo 73:1-28

  • Munthu woopa Mulungu anayambanso kuona zinthu moyenera

    • “Mapazi anga anangotsala pangʼono kusochera” (2)

    • “Ndinkavutika tsiku lonse” (14)

    • ‘Mpaka pamene ndinalowa mʼmalo opatulika a Mulungu’ (17)

    • Anthu oipa ali pamalo oterera (18)

    • Kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino (28)

Nyimbo ya Asafu.+ 73  Mulungu ndi wabwinodi kwa Isiraeli, kwa anthu oyera mtima.+  2  Koma ine mapazi anga anangotsala pangʼono kusochera,Mapazi anga anangotsala pangʼono kuterereka.+  3  Chifukwa ndinkachitira nsanje anthu onyada*Ndikamaona mtendere wa anthu oipa.+  4  Chifukwa samva ululu umene munthu amamva akamafa.Matupi awo amakhala athanzi.*+  5  Iwo savutika ngati mmene anthu ena amavutikira,+Ndipo sakumana ndi mavuto mofanana ndi anthu ena.+  6  Choncho kudzikuza kuli ngati mkanda mʼkhosi mwawo,+Ndipo avala chiwawa ngati malaya.  7  Maso awo akwiririka chifukwa cha kunenepa kwa nkhope yawo.*Ali ndi zinthu zambiri kuposa zimene ankalakalaka mumtima mwawo.  8  Iwo amanyodola komanso kulankhula zinthu zoipa.+ Amaopseza anthu monyada kuti awapondereza.+  9  Amalankhula ngati kuti ali kumwamba,Ndipo malilime awo akuyendayenda padziko lapansi mwamatama. 10  Choncho anthu a Mulungu amawatsatira,Ndipo amamwa madzi awo omwe ndi ambiri. 11  Iwo amanena kuti: “Mulungu angadziwe bwanji?+ Kodi Wamʼmwambamwamba amadziwa chilichonse?” 12  Ndithudi, izi nʼzimene oipa amachita, amakhala mosatekeseka nthawi zonse.+ Iwo amawonjezera chuma chawo.+ 13  Ndithudi, ndayeretsa mtima wanga pachabe,Ndipo ndasamba mʼmanja mwanga pachabe posonyeza kuti ndine wosalakwa.+ 14  Ndinkavutika tsiku lonse,+Ndipo mʼmawa uliwonse ndinkadzudzulidwa.+ 15  Koma ndikananena zinthu zimenezi,Ndikanachitira chinyengo anthu anu.* 16  Nditayesa kuti ndimvetse zimenezi,Zinali zopweteka kwa ine 17  Mpaka pamene ndinalowa mʼmalo opatulika aulemerero a Mulungu,Ndipo ndinazindikira tsogolo lawo. 18  Ndithudi, mwawaika pamalo oterera.+ Mwawagwetsa kuti awonongeke.+ 19  Iwo awonongedwa mwadzidzidzi.+ Afika pamapeto awo modzidzimutsa ndipo atha momvetsa chisoni! 20  Inu Yehova, mofanana ndi maloto amene amaiwalika munthu akadzuka,Inunso mukadzuka mudzawakana.* 21  Koma mtima wanga unandipweteka,+Ndipo mkati mwanga* ndinamva ululu. 22  Ndinali wopanda nzeru ndipo sindinkamvetsa zinthu.Ndinali ngati nyama yosaganiza pamaso panu. 23  Koma tsopano ine ndili ndi inu nthawi zonse.Mwandigwira dzanja langa lamanja.+ 24  Mumanditsogolera ndi malangizo anu,+Ndipo pambuyo pake mudzandipatsa ulemerero.+ 25  Winanso ndi ndani kumwambako amene angandithandize? Ndipo chifukwa chakuti inu muli ndi ine, palibenso chimene ndimalakalaka padziko lapansi.+ 26  Thupi langa ndi mtima wanga zingalefuke,Koma Mulungu ndi thanthwe la mtima wanga ndiponso cholowa changa mpaka kalekale.+ 27  Ndithudi, anthu amene ali kutali ndi inu adzatheratu. Mudzawononga* aliyense amene akukusiyani pochita chigololo.*+ 28  Koma kwa ine, kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino.+ Ndapanga Yehova Ambuye Wamkulu Koposa kukhala malo anga othawirako,Kuti ndilengeze za ntchito zanu zonse.+

Mawu a M'munsi

^ Kapena kuti, “odzitukumula.”
^ Kapena kuti, “Mimba zawo zimakhala zazikulu chifukwa cha kunenepa.”
^ Kapena kuti, “chifukwa choti zinthu zikuwayendera bwino.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mibadwo ya ana anu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mudzawanyoza.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mu impso zanga.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Mudzakhalitsa chete.”
^ Kapena kuti, “pochita zosakhulupirika.”