Salimo 108:1-13

  • Pemphero lopempha kuti awathandize kugonjetsa adani

    • Chipulumutso chochokera kwa munthu nʼchopanda pake (12)

    • “Mulungu adzatipatsa mphamvu” (13)

Nyimbo ndi Salimo la Davide. 108  Ndatsimikiza mtima, Inu Mulungu, Ndidzakuimbirani nyimbo ndi moyo wanga wonse* pogwiritsa ntchito zipangizo zoimbira.+  2  Dzuka, iwe choimbira cha zingwe, ndi iwenso zeze.+ Ine ndidzadzuka mʼbandakucha.  3  Ndidzakutamandani pakati pa mitundu ya anthu, inu Yehova.Ndidzaimba nyimbo zokutamandani pakati pa mitundu ya anthu.  4  Chifukwa chikondi chanu chokhulupirika nʼchachikulu moti chafika kumwamba,+Ndipo kukhulupirika kwanu kwafika kuthambo.  5  Inu Mulungu, kwezekani kupitirira kumwamba.Ulemerero wanu ukhale padziko lonse lapansi.+  6  Kuti anthu amene mumawakonda apulumutsidwe,Tipulumutseni ndi dzanja lanu lamanja ndipo mundiyankhe.+  7  Popeza ndi woyera,* Mulungu walankhula kuti: “Ndidzasangalala popereka Sekemu+ ngati cholowa,Ndipo ndidzayezera anthu anga malo mʼchigwa cha Sukoti.+  8  Giliyadi+ ndi wanga, ngati mmene zilili ndi Manase,Ndipo Efuraimu ndi chipewa* choteteza mutu wanga.+Yuda akuimira mphamvu zanga zolamula.+  9  Mowabu ndi beseni langa losambiramo.+ Edomu ndidzamuponyera nsapato zanga.+ Ndidzafuula mosangalala chifukwa chogonjetsa Filisitiya.”+ 10  Ndi ndani amene adzandibweretse kumzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri? Ndi ndani amene adzanditsogolere mpaka kukafika ku Edomu?+ 11  Kodi si inu Mulungu amene munatikana,Mulungu wathu, amene simukutsogoleranso magulu athu ankhondo?+ 12  Tithandizeni pamene tikukumana ndi mavuto,+Chifukwa chipulumutso chochokera kwa munthu nʼchopanda pake.+ 13  Mulungu adzatipatsa mphamvu,+Ndipo adzapondaponda adani athu.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “ngakhale ndi ulemerero wanga wonse.”
Mabaibulo ena amati, “kumalo ake opatulika.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “malo achitetezo oteteza.”