Salimo 148:1-14

  • Chilengedwe chonse chitamande Yehova

    • “Mutamandeni, inu angelo ake onse” (2)

    • ‘Mutamandeni, inu dzuwa, mwezi ndi nyenyezi’ (3)

    • Ana komanso achikulire atamande Mulungu (12, 13)

148  Tamandani Ya!* Tamandani Yehova inu okhala kumwamba.+Mutamandeni, inu okhala mʼmwamba.   Mutamandeni, inu angelo ake onse.+ Mutamandeni, inu magulu ake onse akumwamba.+   Mutamandeni, inu dzuwa ndi mwezi. Mutamandeni, inu nyenyezi zonse zowala.+   Mutamandeni, inu kumwamba komwe kuli pamwamba kwambiri*Komanso madzi amene ali pamwamba pa kumwamba.   Zonsezi zitamande dzina la Yehova,Chifukwa iye analamula ndipo zinalengedwa.+   Iye amazichititsa kuti zikhalepo kwamuyaya.+Wapereka lamulo limene silidzatha.+   Tamandani Yehova, inu okhala padziko lapansi,Inu zamoyo zikuluzikulu zamʼnyanja komanso inu nonse madzi akuya,   Inu mphezi ndi matalala, sinowo* komanso mitambo yakuda kwambiri,Iwe mphepo yamkuntho, amene umakwaniritsa mawu ake,+   Inu mapiri ndi inu zitunda zonse,+Inu mitengo ya zipatso ndi inu nonse mitengo ya mkungudza.+ 10  Inu nyama zakutchire+ ndi inu nonse nyama zoweta,Inu zinthu zokwawa ndi mbalame zamapiko. 11  Mutamandeni inu mafumu apadziko lapansi komanso inu nonse mitundu ya anthu,Inu akalonga komanso inu oweruza nonse apadziko lapansi,+ 12  Inu anyamata komanso inu atsikana,*Inu achikulire limodzi ndi ana. 13  Anthu komanso zolengedwa zina zonse, atamande dzina la Yehova,Chifukwa dzina lake lokhalo lili pamwamba poti aliyense sangafikepo.+ Ulemerero wake uli pamwamba kuposa dziko lapansi ndi kumwamba.+ 14  Iye adzawonjezera mphamvu* za anthu ake,Kuti anthu ake onse okhulupirika atamandike,Amene ndi ana a Isiraeli, anthu amene ali pafupi ndi iye. Tamandani Ya!*

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
Mʼchiyankhulo choyambirira, “inu kumwamba kwa kumwamba.”
Kapena kuti, “chipale chofewa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anamwali.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzakweza nyanga.”
Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.