Salimo 1:1-6

  • Kusiyanitsa njira ziwiri

    • Wowerenga chilamulo cha Mulungu amakhala wosangalala (2)

    • Olungama ali ngati mtengo wobala zipatso (3)

    • Oipa ali ngati mankhusu amene amauluzika ndi mphepo (4)

1  Wosangalala ndi munthu amene sayenda motsatira malangizo a anthu oipa,Saima mʼnjira ya anthu ochimwa,+Ndipo sakhala pansi pamodzi ndi anthu onyoza.+   Koma amakonda kwambiri chilamulo cha Yehova,+Ndipo amawerenga ndi kuganizira mozama* chilamulocho masana ndi usiku.+   Iye adzakhala ngati mtengo wodzalidwa mʼmbali mwa ngalande za madzi,Umene umabereka zipatso mʼnyengo yake,Umenenso masamba ake safota. Ndipo zonse zimene amachita zimamuyendera bwino.+   Koma si mmene oipa alili.Iwo ali ngati mankhusu* amene amauluzika ndi mphepo.   Nʼchifukwa chake oipa sadzalephera kulangidwa,+Ndipo ochimwa sadzapezekanso pamene pali olungama.+   Chifukwa Yehova amadziwa zochita za olungama,+Koma oipa adzawonongedwa pamodzi ndi zochita zawo.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “ndi kusinkhasinkha.”
“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa popuntha mbewu ngati mpunga ndipo amatha kuuluzika ndi mphepo.