Salimo 91:1-16

  • Kutetezedwa mʼmalo obisika a Mulungu

    • Kupulumutsidwa mumsampha wa wosaka mbalame (3)

    • Kuthawira pansi pa mapiko a Mulungu (4)

    • Kukhala otetezeka ngakhale anthu masauzande atagwa (7)

    • Adzalamula angelo kuti akuteteze (11)

91  Aliyense amene akukhala mʼmalo obisika a Wamʼmwambamwamba+Adzakhala mumthunzi wa Wamphamvuyonse.+  2  Ndidzauza Yehova kuti: “Inu ndinu malo anga othawirako komanso malo anga achitetezo,+Mulungu wanga amene ndimamukhulupirira.”+  3  Chifukwa iye adzakupulumutsa mumsampha wa wosaka mbalame,Komanso ku mliri wowononga.  4  Adzakuphimba ndi mapiko ake,Ndipo udzathawira pansi pa mapiko ake.*+ Kukhulupirika kwake+ kudzakhala chishango chako chachikulu+ komanso khoma lokuteteza.  5  Usiku sudzaopa choopsa chilichonse,+Kapena muvi woponyedwa masana,+  6  Sudzaopa mliri umene umafalikira mumdima,Kapena chiwonongeko chimene chimachitika masana.  7  Anthu 1,000 adzagwa pambali pako,Ndipo anthu 10,000 adzagwa kudzanja lako lamanja.Koma palibe choipa chilichonse chimene chidzakuchitikire.+  8  Maso ako adzaona zimenezi zikuchitika,Pamene anthu oipa akulandira chilango.*  9  Popeza wanena kuti: “Yehova ndi malo anga othawirako,” Wapanga Wamʼmwambamwamba kuti akhale malo ako okhalamo.+ 10  Palibe tsoka limene lidzakugwere,+Ndipo palibe mliri umene udzayandikire tenti yako. 11  Chifukwa adzalamula angelo ake+ zokhudza iwe,Kuti akuteteze mʼnjira zako zonse.+ 12  Iwo adzakunyamula mʼmanja mwawo,+Kuti phazi lako lisawombe mwala.+ 13  Udzapondaponda mkango wamphamvu ndi njoka ya mamba,Ndipo udzapondaponda mkango wamphamvu kwambiri komanso chinjoka chachikulu.+ 14  Mulungu ananena kuti: “Popeza amandikonda,* ine ndidzamupulumutsa.+ Ndidzamuteteza chifukwa akudziwa* dzina langa.+ 15  Adzandiitana ndipo ndidzamuyankha.+ Ndidzakhala naye pa nthawi ya mavuto.+ Ndidzamupulumutsa komanso kumupatsa ulemerero. 16  Ndidzamupatsa moyo wautali,+Ndipo ndidzamuchititsa kuti aone mmene ndidzamupulumutsire.”*+

Mawu a M'munsi

^ Kapena kuti, “Adzakutchinga ndi mapiko ake kuti adani asakuyandikire.”
^ Kapena kuti, “Pamene akubwezera anthu oipa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “wadzigwirizanitsa ndi ine.”
^ Kapena kuti, “akuvomereza.”
^ Kapena kuti, “aone chipulumutso chochokera kwa ine.”