Salimo 143:1-12

  • Kuyembekezera Mulungu ngati dziko louma limene likuyembekezera kuti mvula igwe

    • ‘Ndimaganizira ntchito zanu’ (5)

    • “Ndiphunzitseni kuchita zimene mumafuna” (10)

    • ‘Mzimu wanu umene ndi wabwino unditsogolere’ (10)

Nyimbo ya Davide. 143  Inu Yehova, imvani pemphero langa.+Mvetserani kuchonderera kwanga kopempha thandizo. Ndiyankheni mogwirizana ndi kukhulupirika kwanu komanso chilungamo chanu.  2  Musandiimbe mlandu ine mtumiki wanu,Chifukwa palibe aliyense wamoyo amene angakhale wolungama pamaso panu.+  3  Mdani akundifunafuna.Iye wandipondereza ndipo wandigonjetsa. Wandichititsa kuti ndikhale mumdima ngati anthu amene anafa kalekale.  4  Mphamvu zanga zatha.*+Ndipo mtima wanga wachita dzanzi.+  5  Ndikukumbukira masiku akale.Ndimaganizira mozama zochita zanu zonse.+Ndimaganizira* ntchito ya manja anu ndi mtima wonse.  6  Ine ndikupemphera nditakweza manja anga kwa inu.Ndikuyembekezera inu ngati dziko louma limene likuyembekezera kuti mvula igwe.+ (Selah)  7  Ndiyankheni mofulumira, inu Yehova.+Mphamvu zanga zatha.*+ Musandibisire nkhope yanu,+Chifukwa mukatero ndikhala ngati anthu amene akutsikira kudzenje la manda.+  8  Mʼmawa ndichititseni kumva za chikondi chanu chokhulupirika,Chifukwa ndimadalira inu. Ndidziwitseni njira imene ndikuyenera kuyendamo,+Chifukwa ndimadalira inu kuti muzinditsogolera.*  9  Ndipulumutseni kwa adani anga, inu Yehova. Ine ndikudalira inu kuti munditeteze.+ 10  Ndiphunzitseni kuchita zimene inu mumafuna,+Chifukwa inu ndinu Mulungu wanga. Mzimu wanu ndi wabwino.Unditsogolere mʼmalo otetezeka.* 11  Inu Yehova, ndithandizeni kuti ndikhalebe ndi moyo chifukwa cha dzina lanu. Ndipulumutseni mʼmavuto anga, chifukwa ndinu wachilungamo.+ 12  Chifukwa cha chikondi chanu chokhulupirika, wonongani* adani anga.+Muwononge onse amene akundichitira nkhanza,+Chifukwa ine ndine mtumiki wanu.+

Mawu a M'munsi

^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Mzimu wanga wafooka.”
^ Kapena kuti, “Ndimaphunzira.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Mzimu wanga watha.”
^ Kapena kuti, “Chifukwa ndapereka moyo wanga kwa inu.”
^ Kapena kuti, “Unditsogolere mʼdziko la anthu olungama.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “khalitsani chete.”