FUNSO 15

Kodi Mungatani Kuti Muzikhala Osangalala?

“Ndi bwino kudya zamasamba koma pali chikondi, kusiyana ndi kudya nyama ya ngʼombe yamphongo yonenepa koma pali chidani.”

Miyambo 15:17

“Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino, amene ndimakutsogolerani mʼnjira imene mukuyenera kuyenda.”

Yesaya 48:17

“Osangalala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu chifukwa Ufumu wakumwamba ndi wawo.”

Mateyu 5:3

“Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”

Mateyu 22:39

“Zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.”

Luka 6:31

“Osangalala ndi anthu amene akumva mawu a Mulungu nʼkuwasunga.”

Luka 11:28

“Ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera mʼzinthu zimene ali nazo.”

Luka 12:15

“Choncho, ngati tili ndi chakudya, zovala ndi pogona, tizikhala okhutira ndi zinthu zimenezi.”

1 Timoteyo 6:8

“Kupatsa kumatichititsa kukhala osangalala kwambiri kuposa kulandira.”

Machitidwe 20:35