Salimo 101:1-8
Nyimbo ndi Salimo la Davide.
101 Ndidzaimba za chikondi chokhulupirika komanso chilungamo chanu.
Inu Yehova, ndidzakuimbirani nyimbo zokutamandani.
2 Ndidzachita zinthu mwanzeru komanso mosalakwitsa kanthu.*
Kodi mudzandithandiza liti?
Ndidzayenda mʼnyumba yanga ndi mtima wokhulupirika.+
3 Sindidzayangʼana chinthu chilichonse choipa.*
Ndimadana ndi zochita za anthu amene asiya kuchita zinthu zabwino.+Sindidzalola kuti zochita zawozo zindikhudze.
4 Aliyense wopotoka maganizo, ali kutali ndi ine.Sindidzalola* kuchita zinthu zoipa.
5 Aliyense wonenera mnzake miseche,+Ndidzamukhalitsa chete.*
Aliyense amene ali ndi mtima wonyada komanso wodzikweza,Sindidzamulekerera.
6 Ndidzayangʼana anthu okhulupirika kwa inu padziko lapansi,Kuti azikhala ndi ine.
Amene akuyenda mosalakwitsa kanthu* adzanditumikira.
7 Mʼnyumba yanga simudzakhala munthu wachinyengo,Ndipo wabodza aliyense sadzaima pamaso panga.
8 Mʼmawa uliwonse ndidzawononga* oipa onse apadziko lapansi,Ndidzapha onse ochita zoipa nʼkuwachotsa mumzinda wa Yehova.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “komanso mokhulupirika.”
^ Kapena kuti, “chopanda pake.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Sindidzadziwa.”
^ Kapena kuti, “Ndidzathana naye.”
^ Kapena kuti, “akuyenda mokhulupirika.”
^ Kapena kuti, “ndidzathana ndi.”