Salimo 11:1-7

  • Kuthawira kwa Yehova

    • “Yehova ali mʼkachisi wake wopatulika” (4)

    • Mulungu amadana ndi aliyense wokonda chiwawa (5)

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide. 11  Ine ndathawira kwa Yehova.+ Ndiye nʼchifukwa chiyani mukundiuza kuti: “Thawira kuphiri ngati mbalame!   Onani mmene anthu oipa akungira uta,Aika mivi yawo pa chingwe cha uta,Kuti alase anthu owongoka mtima kuchokera pamalo amdima.   Kodi munthu wolungama angachite chiyaniMaziko achilungamo atagumulidwa?”   Yehova ali mʼkachisi wake wopatulika.+ Mpando wachifumu wa Yehova uli kumwamba.+ Maso ake amaona, inde maso ake* amayangʼanitsitsa ana a anthu.+   Yehova amayangʼanitsitsa munthu wolungama komanso munthu woipa.+Mulungu amadana ndi aliyense amene amakonda chiwawa.+   Oipa, iye adzawagwetsera misampha* ngati mvula.Moto ndi sulufule+ komanso mphepo yotentha zidzakhala chakumwa chawo.   Chifukwa Yehova ndi wolungama.+ Iye amakonda ntchito zolungama.+ Anthu owongoka mtima adzaona nkhope yake.*+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “maso ake owala.”
Mabaibulo ena amati, “makala amoto.”
Kapena kuti, “adzawakomera mtima.”