Salimo 50:1-23
Nyimbo ya Asafu.+
50 Yehova, Mulungu wa milungu+ walankhula.Iye akuitana anthu onse okhala padziko lapansi,Kuchokera kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera.*
2 Mulungu wawala ali ku Ziyoni, mzinda wokongola kwambiri.+
3 Mulungu wathu adzabwera ndipo sangakhale chete.+
Pamaso pake pali moto wowononga,+Ndipo pamalo onse omuzungulira pali chimphepo chamkuntho.+
4 Akuitana kumwamba ndi dziko lapansi+Kuti aweruze anthu ake. Iye akuti:+
5 “Sonkhanitsani okhulupirika anga kwa ine,Amene akuchita pangano ndi ine pogwiritsa ntchito nsembe.”+
6 Kumwamba kukulengeza kuti iye ndi wachilungamo,Chifukwa Mulungu ndi Woweruza.+ (Selah)
7 “Ndimvereni anthu anga, ndipo ine ndilankhula,Inu Aisiraeli, ine ndipereka umboni wotsutsana nanu.+
Ine ndine Mulungu, Mulungu wanu.+
8 Sindikukudzudzulani chifukwa cha nsembe zanu,Kapena chifukwa cha nsembe zanu zopsereza zathunthu zimene mumapereka kwa ine nthawi zonse.+
9 Sindikuyenera kutenga ngʼombe yamphongo mʼnyumba yanu,Kapena mbuzi* mʼmakola anu.+
10 Chifukwa nyama iliyonse yakutchire ndi yanga,+Ngakhale nyama zopezeka mʼmapiri 1,000.
11 Ndikudziwa mbalame iliyonse ya mʼmapiri,+Nyama zosawerengeka zakutchire ndi zanga.
12 Ngakhale nditakhala ndi njala, sindingakuuzeni,Chifukwa dziko lonse ndiponso zonse zimene zili mmenemo ndi zanga.+
13 Kodi ndiyenera kudya nyama ya ngʼombe zamphongoKapena kumwa magazi a mbuzi?+
14 Yamikani Mulungu kuti ikhale ngati nsembe imene mukupereka kwa iye,+Ndipo perekani kwa Wamʼmwambamwamba zimene mwalonjeza.+
15 Pa nthawi yamavuto mundiitane.+
Ine ndidzakupulumutsani, ndipo inu mudzandilemekeza.”+
16 Koma Mulungu adzauza woipa kuti:
“Ndi ndani wakupatsa udindo wofotokoza malangizo anga,+Kapena wolankhula za pangano langa?+
17 Iwe umadana ndi chilango,*Ndipo sumamvera mawu anga.*+
18 Ukaona wakuba umasangalala ndi zochita zake.*+Ndipo umagwirizana ndi anthu achigololo.
19 Umagwiritsa ntchito pakamwa pako kufalitsa zinthu zoipa,Ndipo lilime lako limalankhula zachinyengo.+
20 Umakhala pansi nʼkumanenera mʼbale wako zinthu zoipa,+Umaulula zolakwa za* mwana wamwamuna wa mayi ako.
21 Utachita zinthu zimenezi, ine sindinalankhule kanthu,Choncho unkaganiza kuti ndikuona zinthu ngati mmene iweyo ukuzionera.
Koma tsopano ndikudzudzulaNdipo ndikuuza mlandu umene ndakupeza nawo.+
22 Ganizirani zinthu zimenezi, anthu oiwala Mulungu inu,+Kuti ndisakukhadzulekhadzuleni popanda aliyense wokupulumutsani.
23 Amene akundiyamikira kuti ikhale nsembe imene akupereka kwa ine akundilemekeza.+Ndipo munthu amene akupitiriza kuchita zabwino,Ndidzamuonetsa chipulumutso changa.”+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Kuchokera kumʼmawa mpaka kumadzulo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbuzi zamphongo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “umaponya mawu anga kunkhongo.”
^ Kapena kuti, “malangizo.”
^ Mabaibulo ena amati, “umamutsatira.”
^ Kapena kuti, “Umaipitsa mbiri ya.”