Salimo 10:1-18
ל [Lamed]
10 Nʼchifukwa chiyani inu Yehova mukuima kutali?
Nʼchifukwa chiyani mukubisala pa nthawi ya mavuto?+
2 Modzikuza, munthu woipa amathamangitsa munthu wovutika,+Koma adzakodwa mumsampha wa ziwembu zake.+
3 Chifukwa munthu woipa amanena za zolinga zake* zadyera modzitamandira,+Ndipo amadalitsa munthu wadyera.נ [Nun]Iye amanyoza Yehova.
4 Chifukwa cha kudzikweza, munthu woipa safufuza kuti adziwe Mulungu.Iye amangoganiza kuti: “Kulibe Mulungu.”+
5 Zochita zake zikupitiriza kumuyendera bwino,+Koma zigamulo zanu sangathe kuzimvetsa.+Iye amanyogodola adani ake onse.
6 Mumtima mwake amanena kuti: “Sindidzagwedezeka.*Ku mibadwomibadwo,Tsoka silidzandigwera.”+
פ [Pe]
7 Mʼkamwa mwake mwadzaza matemberero, mabodza ndi kuopseza ena.+Pansi pa lilime lake pali mavuto ndi zopweteka ena.+
8 Iye amabisalira anthu pafupi ndi midzi.Amachoka pamene wabisalapo nʼkupha munthu wosalakwa.+
ע [Ayin]
Maso ake akuyangʼanayangʼana munthu woti amuchite chiwembu.+
9 Amadikirira anthu pamalo amene iye amabisala ngati mkango umene uli pamalo ake amene umabisala.*+
Amadikirira kuti agwire munthu wovutika.
Amagwira munthu wovutikayo pomukulunga ndi ukonde wake.+
10 Munthu wovutikayo amaponderezedwa ndipo amawerama ndi chisoni.Anthu ovutikawo amagwidwa ndi dzanja lake lamphamvu.
11 Mumtima mwake amanena kuti: “Mulungu waiwala zoipa zimene ndimachita.+
Iye wayangʼana kumbali.
Sakuona chilichonse.”+
ק [Qoph]
12 Nyamukani, inu Yehova.+ Inu Mulungu, chitanipo kanthu.+
Musaiwale anthu ovutika.+
13 Nʼchifukwa chiyani munthu woipa wanyoza Mulungu?
Mumtima mwake amanena kuti: “Simudzandiimba mlandu.”
ר [Resh]
14 Koma inu mumaona mavuto ndi masautso.
Mumayangʼana nʼkuchitapo kanthu.+
Munthu wovutika amayangʼana kwa inu,+Mumathandiza mwana wamasiye.+
ש [Shin]
15 Thyolani dzanja la munthu woipa ndi wankhanza,+Kuti mukamafufuza zoipa zakeMusazipezenso.
16 Yehova ndi Mfumu mpaka kalekale.+
Mitundu ya anthu yawonongedwa, yachotsedwa padziko lapansi.+
ת [Taw]
17 Koma inu Yehova mudzamva pempho la anthu ofatsa.+
Mudzalimbitsa mitima yawo+ ndipo mudzawamvetsera mwatcheru.+
18 Mudzaweruza mwachilungamo mwana wamasiye komanso anthu oponderezedwa,+Kuti munthu wamba wochokera kufumbi asadzawachititsenso mantha.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “za zokhumba za moyo wake.”
^ Kapena kuti, “Sindidzadzandira.”
^ Kapena kuti, “uli paziyangoyango.”