Salimo 110:1-7

  • Mfumu komanso wansembe ngati Melekizedeki

    • ‘Ukalamulire pakati pa adani ako’ (2)

    • Achinyamata odzipereka ali ngati mame (3)

Salimo ndi Nyimbo ya Davide. 110  Yehova anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja+Mpaka nditaika adani ako kuti akhale chopondapo mapazi ako.”+   Yehova adzatambasula ndodo yako yachifumu kuti ulamulirenso madera ena osati mu Ziyoni mokha. Iye adzanena kuti: “Pita pakati pa adani ako ndipo ukawagonjetse.”+   Anthu ako adzadzipereka mofunitsitsa pa tsiku limene udzatsogolera asilikali ako kunkhondo.* Gulu la achinyamata amene ali ngati mame amʼbandakucha likukuthandiza.Iwo ndi apadera kwa ine komanso ndi okongola.   Yehova walumbira ndipo sadzasintha maganizo. Iye wati: “Iwe ndiwe wansembe mpaka kalekale,+Mofanana ndi unsembe wa Melekizedeki!”+   Yehova adzakhala kudzanja lako lamanja.+Iye adzaphwanya mafumu pa tsiku la mkwiyo wake.+   Adzapereka chiweruzo ku* mitundu ya anthu.+Adzachititsa kuti mʼdziko mudzaze mitembo ya anthu.+ Adzaphwanya mtsogoleri* wa dziko lalikulu.*   Ali mʼnjira, iye* adzamwa madzi amumtsinje. Choncho adzatukula kwambiri mutu wake.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “pa tsiku limene asilikali ako adzakonzekere kumenya nkhondo.”
Kapena kuti, “pakati pa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mutu.”
Kapena kuti, “wa dziko lonse lapansi.”
Kutanthauza, “Ambuye wanga” amene atchulidwa mu vesi 1.