FUNSO 13

Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani ya Ntchito?

“Kodi wamuona munthu waluso pa ntchito yake? Iye adzaima pamaso pa mafumu. Sadzaima pamaso pa anthu wamba.”

Miyambo 22:29

“Munthu wakuba asiye kubako, koma azigwira ntchito molimbikira. Azigwira ntchito yabwino ndi manja ake kuti azitha kupeza zinthu zimene angathe kugawana ndi munthu wosowa.”

Aefeso 4:28

“Munthu aliyense adye ndi kumwa nʼkumasangalala ndi zinthu zabwino, chifukwa cha ntchito yake yonse imene waigwira mwakhama. Imeneyi ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.”

Mlaliki 3:13