Salimo 119:1-176
-
Kuyamikira mawu amtengo wapatali a Mulungu
-
“Kodi wachinyamata angakhale bwanji woyera pa moyo wake?” (9)
-
“Ndimakonda kwambiri zikumbutso zanu” (24)
-
“Ndimakonda kwambiri chilamulo chanu!” (97)
-
“Wozindikira kwambiri kuposa aphunzitsi anga onse” (99)
-
“Mawu anu ndi nyale younikira kumapazi anga” (105)
-
“Mawu anu onse ndi choonadi chokhachokha” (160)
-
Amene amakonda chilamulo cha Mulungu amakhala ndi mtendere (165)
-
א [Aleph]
119 Osangalala ndi anthu amene salakwitsa kanthu* mʼnjira zawo,Amene amatsatira chilamulo cha Yehova.+
2 Osangalala ndi anthu amene amasunga zikumbutso zake,+Amene amamufunafuna ndi mtima wawo wonse.+
3 Iwo sachita zinthu zosalungama.Amayenda mʼnjira zake.+
4 Inu mwalamulaKuti tizitsatira malamulo anu mosamala.+
5 Zikanakhala bwino ndikanakhala wolimba*+Kuti nditsatire malangizo anu.
6 Zikanatero sindikanachita manyazi,+Pa nthawi imene ndikuganizira malamulo anu onse.
7 Ndidzakutamandani ndi mtima wowongoka,Pamene ndikuphunzira zigamulo zanu zolungama.
8 Ndidzasunga malangizo anu.
Choncho musandisiye ndekha.
ב [Beth]
9 Kodi wachinyamata angakhale bwanji woyera pa moyo wake?
Akamadzifufuza nthawi zonse kuti aone ngati zochita zake zikugwirizana ndi mawu anu.+
10 Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse.
Musalole kuti ndisochere nʼkuchoka pa malamulo anu.+
11 Ndasunga mosamala mawu anu mumtima mwanga+Kuti ndisakuchimwireni.+
12 Mutamandike, inu Yehova.Ndiphunzitseni malamulo anu.
13 Ndi milomo yanga ndalengezaZigamulo zonse zimene inu mwanena.
14 Ndimasangalala ndi zikumbutso zanu,+Kuposa mmene ndimasangalalira ndi zinthu zina zonse zamtengo wapatali.+
15 Ndidzaganizira mozama* malamulo anu,+Ndipo ndidzayangʼanitsitsa njira zanu.+
16 Ndimakonda malamulo anu.
Sindidzaiwala mawu anu.+
ג [Gimel]
17 Ndichitireni zinthu mokoma mtima, ine mtumiki wanu,Kuti ndikhale ndi moyo komanso kuti ndisunge mawu anu.+
18 Tsegulani maso anga kuti ndione bwinobwinoZinthu zodabwitsa zamʼchilamulo chanu.
19 Ine ndine mlendo mʼdzikoli.+
Musandibisire malamulo anu.
20 Ndimalakalaka kwambiriNditadziwa zigamulo zanu nthawi zonse.
21 Mumadzudzula anthu odzikuza,Otembereredwa amene akusochera nʼkusiya kutsatira malamulo anu.+
22 Muwachititse kuti asiye* kusandilemekeza komanso kundinyoza,Chifukwa ndatsatira zikumbutso zanu.
23 Ngakhale pamene akalonga asonkhana pamodzi nʼkumakambirana zoti andiukire,Ine mtumiki wanu ndimaganizira mozama* malangizo anu.
24 Ndimakonda kwambiri zikumbutso zanu,+Ndipo zili ngati anthu amene amandipatsa malangizo.+
ד [Daleth]
25 Ndagona pafumbi.+
Ndithandizeni kuti ndikhalebe ndi moyo mogwirizana ndi mawu anu.+
26 Ndinakuuzani za njira zanga ndipo munandiyankha.Ndiphunzitseni malamulo anu.+
27 Ndithandizeni kumvetsa tanthauzo la* malamulo anu,Kuti ndiganizire mozama* ntchito zanu zodabwitsa.+
28 Ine ndakhala ndikusowa tulo chifukwa cha chisoni.
Ndilimbitseni mogwirizana ndi mawu anu.
29 Ndithandizeni kuti ndisakhale munthu wachinyengo,+Ndipo mundikomere mtima pondipatsa chilamulo chanu.
30 Ine ndasankha kuti ndizichita zinthu mokhulupirika.+
Ndimadziwa kuti zigamulo zanu ndi zolungama.
31 Ndimatsatira zikumbutso zanu nthawi zonse.+
Inu Yehova, musalole kuti ndikhumudwe.*+
32 Ndidzatsatira* malamulo anu ndi mtima wonse,Chifukwa mwandithandiza kuti ndiwamvetse bwino.
ה [He]
33 Ndiphunzitseni inu Yehova,+ kuti ndizichita zinthu mogwirizana ndi malangizo anu,Ndipo ndidzawatsatira kwa moyo wanga wonse.+
34 Ndithandizeni kuti ndikhale wozindikiraKuti nditsatire chilamulo chanu,Ndiponso kuti ndichisunge ndi mtima wanga wonse.
35 Nditsogolereni* mʼnjira ya malamulo anu,+Chifukwa njira imeneyi imandisangalatsa
36 Ndithandizeni kuti mtima wanga uzikonda zikumbutso zanu,Osati kupeza phindu mwachinyengo.+
37 Ndithandizeni kuti ndizipewa kuyangʼana zinthu zopanda pake.+Ndithandizeni kuyenda mʼnjira yanu kuti ndikhalebe ndi moyo.
38 Kwaniritsani zimene munalonjeza* mtumiki wanu,Kuti anthu azikuopani.
39 Chotsani zinthu zochititsa manyazi zimene ndikuziopa,Chifukwa zigamulo zanu ndi zabwino.+
40 Taonani mmene ndikulakalakira malamulo anu.
Ndithandizeni kukhalabe ndi moyo mogwirizana ndi chilungamo chanu.
ו [Waw]
41 Ndione chikondi chanu chokhulupirika, inu Yehova,+Komanso mundipulumutse mogwirizana ndi lonjezo lanu.*+
42 Mukatero ndiyankha amene akundinyoza,Chifukwa ine ndimadalira mawu anu.
43 Ndithandizeni kuti ndipitirize kunena mawu a choonadi,Chifukwa ndikuyembekezera* chigamulo chanu.
44 Ndidzasunga chilamulo chanu nthawi zonse,Mpaka kalekale.+
45 Ndidzayendayenda mʼmalo otetezeka,*+Chifukwa ndimayesetsa kuphunzira malamulo anu.
46 Ndidzanena zokhudza zikumbutso zanu pamaso pa mafumu,Ndipo sindidzachita manyazi.+
47 Ndimakonda kwambiri malamulo anu,Inde, ndimawakonda.+
48 Ndidzapemphera kwa inu nditakweza manja anga chifukwa ndimakonda malamulo anu,+Ndipo ndidzaganizira mozama* malangizo anu.+
ז [Zayin]
49 Kumbukirani mawu amene* munandiuza ine mtumiki wanu,Mawu amene mumandipatsa nawo chiyembekezo.*
50 Izi ndi zimene zimandilimbikitsa ndikakhala pamavuto,+Chifukwa mawu anu andithandiza kuti ndikhalebe ndi moyo.
51 Anthu odzikuza andinyoza koopsa.Koma ine sindinasiye kutsatira chilamulo chanu.+
52 Ndimakumbukira zigamulo zanu zakalekale+ inu Yehova,Ndipo zimandilimbikitsa.+
53 Ndakwiya kwambiri chifukwa cha oipa,Amene akusiya chilamulo chanu.+
54 Kwa ine, malangizo anu ali ngati nyimbo,Kulikonse kumene ndimakhala.*
55 Usiku ndimakumbukira dzina lanu, inu Yehova,+Kuti ndisunge chilamulo chanu.
56 Ndakhala ndikuchita zimeneziChifukwa ndimatsatira malamulo anu.
ח [Heth]
57 Yehova ndi cholowa changa.+Ndalonjeza kusunga mawu anu.+
58 Ndikukupemphani* ndi mtima wanga wonse.+Ndikomereni mtima+ mogwirizana ndi zimene munalonjeza.*
59 Ndaganizira mozama za njira zanga,Kuti mapazi anga ndiwabwezere ku zikumbutso zanu.+
60 Ndimafulumira ndipo sindizengerezaKusunga malamulo anu.+
61 Zingwe za oipa zandikulunga,Koma ine sindinaiwale chilamulo chanu.+
62 Ndimadzuka pakati pa usiku kuti ndikuyamikeni+Chifukwa cha zigamulo zanu zolungama.
63 Ine ndine mnzawo wa anthu amene amakuopani,Ndiponso wa anthu amene amasunga malamulo anu.+
64 Inu Yehova, chikondi chanu chokhulupirika chadzaza dziko lapansi.+Ndiphunzitseni malamulo anu.
ט [Teth]
65 Inu Yehova, mwandichitira zabwino ine mtumiki wanu,Mogwirizana ndi mawu anu.
66 Ndithandizeni kuti ndikhale wozindikira komanso wodziwa zinthu,+Chifukwa ndimadalira malamulo anu.
67 Ndisanakumane ndi mavuto ndinkasochera pafupipafupi,*Koma panopa ndimasunga mawu anu.+
68 Inu ndinu wabwino+ ndipo ntchito zanu ndi zabwino.
Ndiphunzitseni malamulo anu.+
69 Anthu odzikuza akundinenera zinthu zambiri zabodza,Koma ine ndimasunga malamulo anu ndi mtima wanga wonse.
70 Mitima yawo yauma ngati mwala,*+Koma ine ndimakonda kwambiri chilamulo chanu.+
71 Zili bwino kuti ndakumana ndi mavuto,+Kuti ndiphunzire malamulo anu.
72 Chilamulo chimene mwapereka nʼchabwino kwa ine,+Nʼchabwino kwambiri kuposa ndalama zagolide ndi zasiliva masauzande ambiri.+
י [Yod]
73 Manja anu anandipanga komanso kundiumba.
Ndithandizeni kuti ndikhale wozindikira,Kuti ndiphunzire malamulo anu.+
74 Amene amakuopani amasangalala akandiona,Chifukwa mawu anu ndi chiyembekezo changa.*+
75 Inu Yehova, ndikudziwa kuti zigamulo zanu ndi zolungama+Komanso kuti mwandilanga chifukwa chakuti ndinu wokhulupirika.+
76 Chikondi chanu chokhulupirika+ chindilimbikitse,Mogwirizana ndi zimene munandilonjeza* ine mtumiki wanu.
77 Ndisonyezeni chifundo kuti ndipitirize kukhala ndi moyo,+Chifukwa ndimakonda kwambiri chilamulo chanu.+
78 Odzikuza achite manyazi,Chifukwa amandilakwira popanda chifukwa.
Koma ine ndidzaganizira mozama* malamulo anu.+
79 Anthu amene amakuopani abwerere kwa ine,Amene amadziwa zikumbutso zanu.
80 Mtima wanga uzitsatira malangizo anu mosalakwitsa kanthu,+Kuti ndisachite manyazi.+
כ [Kaph]
81 Ine ndikulakalaka chipulumutso chanu,+Chifukwa mawu anu ndi chiyembekezo changa.*
82 Maso anga akulakalaka mawu anu+Ndipo ndikunena kuti: “Kodi mudzandilimbikitsa liti?”+
83 Chifukwa ndili ngati thumba lachikopa limene lauma mu utsi,Koma sindinaiwale malangizo anu.+
84 Kodi ine mtumiki wanu ndidikira mpaka liti?
Kodi anthu amene akundizunza mudzawaweruza liti?+
85 Anthu odzikuza andikumbira dzenje kuti ndigweremo,Anthu amene safuna kutsatira chilamulo chanu.
86 Malamulo anu onse ndi odalirika.
Anthu akundizunza popanda chifukwa. Chonde, ndithandizeni.+
87 Iwo anangotsala pangʼono kundifafaniza padziko lapansi,Koma ine sindinasiye kutsatira malamulo anu.
88 Ndithandizeni kuti ndikhalebe ndi moyo chifukwa cha chikondi chanu chokhulupirika,Kuti ndisunge zikumbutso zimene mwatipatsa.
ל [Lamed]
89 Inu Yehova, mawu anu adzakhazikika kumwamba,+Mpaka kalekale.
90 Kukhulupirika kwanu kudzakhalapobe ku mibadwo yonse.+
Mwakhazikitsa mwamphamvu dziko lapansi, kuti lipitirizebe kukhalapo.+
91 Ntchito zanu zilipobe mpaka pano chifukwa cha zigamulo zanu,Chifukwa zonsezo zimakutumikirani.
92 Ndikanakhala kuti sindimakonda kwambiri chilamulo chanu,Ndikanakhala nditafa chifukwa cha mavuto anga.+
93 Sindidzaiwala malamulo anu,Chifukwa mwandithandiza kuti ndikhalebe ndi moyo pogwiritsa ntchito malamulo amenewo.+
94 Ine ndine wanu. Chonde ndipulumutseni,+Chifukwa ndimayesetsa kuphunzira malamulo anu.+
95 Oipa amayembekezera kuti andiwononge,Koma ine ndimamvetsera mwatcheru zikumbutso zanu.
96 Ndaona kuti zinthu zonse zabwino kwambiri zili ndi malire,Koma malamulo anu alibe malire.*
מ [Mem]
97 Ndimakonda kwambiri chilamulo chanu!+
Ndimaganizira mozama* chilamulocho tsiku lonse.+
98 Malamulo anu amandichititsa kukhala wanzeru kuposa adani anga,+Chifukwa ali ndi ine mpaka kalekale.
99 Ndine wozindikira kwambiri kuposa aphunzitsi anga onse,+Chifukwa ndimaganizira mozama* zikumbutso zanu.
100 Ndimachita zinthu mozindikira kuposa anthu achikulire,Chifukwa ndimatsatira malamulo anu.
101 Ndimakana kuyenda mʼnjira iliyonse yoipa,+Kuti ndisunge mawu anu.
102 Sindinasiye kutsatira zigamulo zanu,Chifukwa inu mwandilangiza.
103 Mawu anu amatsekemera kwambiri mʼkamwa mwanga,Kuposa mmene uchi umakomera!+
104 Ndimachita zinthu mozindikira chifukwa cha malamulo anu.+
Nʼchifukwa chake ndimadana ndi njira iliyonse yachinyengo.+
נ [Nun]
105 Mawu anu ndi nyale younikira kumapazi anga,Komanso kuwala kounikira njira yanga.+
106 Ndalumbira kuti ndidzasunga zigamulo zanu zolungama,Ndipo ndidzakwaniritsa lumbiro langa.
107 Ndavutika kwambiri.+
Inu Yehova, ndithandizeni kuti ndikhalebe ndi moyo mogwirizana ndi mawu anu.+
108 Inu Yehova, chonde sangalalani ndi nsembe zanga zaufulu zokutamandani,*+Ndipo mundiphunzitse zigamulo zanu.+
109 Nthawi zonse moyo wanga umakhala pangozi,*Koma sindinaiwale chilamulo chanu.+
110 Oipa anditchera msampha,Koma ine sindinasochere nʼkusiya kutsatira malamulo anu.+
111 Ndimaona kuti zikumbutso zanu ndi chuma changa mpaka kalekale,*Chifukwa zimasangalatsa mtima wanga.+
112 Ndatsimikiza mtima kumvera malamulo anuNthawi zonse, mpaka ndidzamwalire.
ס [Samekh]
113 Ndimadana ndi anthu amitima iwiri,+Koma ndimakonda chilamulo chanu.+
114 Inu ndinu malo anga obisalamo komanso chishango changa,+Chifukwa mawu anu ndi chiyembekezo changa.*+
115 Mukhale kutali ndi ine, anthu oipa inu,+Kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga.
116 Inu Mulungu, ndithandizeni mogwirizana ndi zimene munalonjeza,*+Kuti ndikhalebe ndi moyo.Musalole kuti ndichite manyazi chifukwa cha chiyembekezo changa.*+
117 Ndithandizeni kuti ndipulumutsidwe.+Mukatero ndidzamvera malangizo anu nthawi zonse.+
118 Onse amene amasochera nʼkusiya kutsatira malangizo anu mumawakana,+Chifukwa ndi abodza komanso achinyengo.
119 Anthu onse oipa apadziko lapansi mumawataya ngati zinthu zopanda ntchito zimene zimatsalira poyenga zitsulo.+
Nʼchifukwa chake ine ndimakonda zikumbutso zanu.
120 Chifukwa choopa inu, thupi langa limanjenjemera.Ndikuopa zigamulo zanu.
ע [Ayin]
121 Ndachita zinthu zachilungamo komanso zoyenera.
Musandipereke kwa anthu amene amandipondereza.
122 Lonjezani kuti mudzandithandiza ine mtumiki wanu.Musalole kuti anthu odzikuza andipondereze.
123 Maso anga afooka chifukwa choyembekezera chipulumutso chanu+Komanso malonjezo* anu olungama.+
124 Ndisonyezeni chikondi chanu chokhulupirika ine mtumiki wanu,+Ndipo ndiphunzitseni malamulo anu.+
125 Ine ndine mtumiki wanu. Ndithandizeni kukhala wozindikira,+Kuti ndidziwe zikumbutso zanu.
126 Nthawi yoti Yehova achitepo kanthu yakwana,+Chifukwa iwo aphwanya chilamulo chanu.
127 Nʼchifukwa chake ine ndimakonda malamulo anuKuposa golide, ngakhale golide wabwino kwambiri.*+
128 Choncho ndimaona kuti malangizo* onse ochokera kwa inu ndi abwino.+Ndimadana ndi njira iliyonse yachinyengo.+
פ [Pe]
129 Zikumbutso zanu nʼzodabwitsa.
Nʼchifukwa chake ine ndimazitsatira.
130 Mawu anu akafotokozedwa amathandiza munthu kuti akhale wozindikira,+Amathandiza munthu wosadziwa zambiri kuti akhale wozindikira.+
131 Ndatsegula kwambiri pakamwa panga kuti ndiuse moyo,*Chifukwa ndikulakalaka malamulo anu.+
132 Ndiyangʼaneni ndipo mundikomere mtima,+Mogwirizana ndi zigamulo zimene mumapereka kwa anthu amene amakonda dzina lanu.+
133 Nditsogolereni ndi mawu anu kuti ndiyende mʼnjira yotetezeka.Musalole kuti choipa chilichonse chindilamulire.+
134 Ndipulumutseni* kwa anthu amene akundipondereza,Ndipo ine ndidzasunga malamulo anu.
135 Chititsani nkhope yanu kuti indiwalire* ine mtumiki wanu,+Ndipo mundiphunzitse malamulo anu.
136 Misozi ikutsika mʼmaso mwanga ngati mtsinjeChifukwa anthu sakusunga chilamulo chanu.+
צ [Tsade]
137 Ndinu wolungama, inu Yehova,+Ndipo zigamulo zanu ndi zachilungamo.+
138 Zikumbutso zimene mumapereka ndi zolungamaKomanso nʼzodalirika kwambiri.
139 Kudzipereka kwanga kwa inu kuli ngati moto umene ukuyaka mumtima mwanga,+Chifukwa adani anga aiwala mawu anu.
140 Mawu anu ndi oyengeka bwino kwambiri,+Ndipo ine mtumiki wanu ndimawakonda.+
141 Anthu ena amandiona ngati wopanda ntchito komanso wonyozeka.+Komabe sindinaiwale malamulo anu.
142 Chilungamo chanu chidzakhalapo mpaka kalekale,+Ndipo chilamulo chanu ndi choonadi.+
143 Ngakhale kuti ndikukumana ndi zowawa komanso mavuto,Ndikupitirizabe kukonda malamulo anu.
144 Zikumbutso zanu zidzakhalabe zolungama mpaka kalekale.
Ndithandizeni kukhala wozindikira+ kuti ndikhalebe ndi moyo.
ק [Qoph]
145 Ndaitana ndi mtima wanga wonse. Ndiyankheni inu Yehova.
Ndidzatsatira malangizo anu.
146 Ndakuitanani. Ndipulumutseni chonde!
Ndidzasunga zikumbutso zanu.
147 Ndadzuka mʼbandakucha kuti ndipemphe thandizo kwa inu,+Chifukwa mawu anu ndi chiyembekezo changa.*
148 Ndimadzuka pakati pa usiku,*Kuti ndiganizire mozama* mawu anu.+
149 Imvani mawu anga chifukwa cha chikondi chanu chokhulupirika.+
Inu Yehova, ndithandizeni kuti ndikhalebe ndi moyo mogwirizana ndi chilungamo chanu.
150 Anthu amene amakonda kuchita khalidwe lochititsa manyazi* abwera pafupi ndi ine.Iwo ndi otalikirana kwambiri ndi chilamulo chanu.
151 Inu Yehova muli pafupi,+Ndipo malamulo anu onse ndi choonadi.+
152 Kale kwambiri, ndinaphunzira zokhudza zikumbutso zanu,Kuti munazikhazikitsa kuti zikhalepo mpaka kalekale.+
ר [Resh]
153 Onani mavuto anga ndipo mundipulumutse,+Chifukwa sindinaiwale chilamulo chanu.
154 Nditetezeni pa mlandu wanga* ndipo mundipulumutse.+Ndithandizeni kuti ndikhalebe ndi moyo mogwirizana ndi lonjezo lanu.*
155 Chipulumutso chili kutali kwambiri ndi anthu oipa,Chifukwa sanaphunzire malamulo anu.+
156 Chifundo chanu nʼchachikulu, inu Yehova.+
Ndithandizeni kuti ndikhalebe ndi moyo mogwirizana ndi chilungamo chanu.
157 Anthu ondizunza komanso adani anga ndi ambiri.+Koma ine sindinasiye kutsatira zikumbutso zanu.
158 Ndimanyansidwa ndi anthu ochita zinthu mwachinyengo,Chifukwa sasunga mawu anu.+
159 Onani mmene ndimakondera malamulo anu.
Inu Yehova, ndithandizeni kuti ndikhalebe ndi moyo chifukwa cha chikondi chanu chokhulupirika.+
160 Mawu anu onse ndi choonadi chokhachokha,+Ndipo zigamulo zanu zonse zolungama zidzakhalapo mpaka kalekale.
ש [Sin] kapena kuti [Shin]
161 Akalonga amandizunza+ popanda chifukwa,Koma mtima wanga umaopa mawu anu.+
162 Ndimasangalala ndi mawu anu,+Mofanana ndi munthu amene wapeza chuma chambiri.
163 Ndimadana ndi chinyengo ndipo chimandinyansa,+Ndimakonda chilamulo chanu.+
164 Ndimakutamandani maulendo 7 pa tsiku,Chifukwa cha zigamulo zanu zolungama.
165 Anthu amene amakonda chilamulo chanu amakhala ndi mtendere wochuluka,+Palibe chimene chingawakhumudwitse.*
166 Ndimayembekezera ntchito zanu zachipulumutso, inu Yehova,Ndipo ndimatsatira malamulo anu.
167 Ndimasunga zikumbutso zanu,Ndipo ndimazikonda kwambiri.+
168 Ndimasunga malamulo anu ndi zikumbutso zanu,Chifukwa inu mukudziwa zinthu zonse zimene ndimachita.+
ת [Taw]
169 Inu Yehova, imvani kulira kwanga kopempha thandizo.+
Ndithandizeni kuti ndikhale wozindikira, mogwirizana ndi mawu anu.+
170 Pempho langa lakuti mundikomere mtima lifike kwa inu.
Ndipulumutseni mogwirizana ndi zimene munalonjeza.*
171 Milomo yanga isefukire ndi mawu okutamandani,+Chifukwa mumandiphunzitsa malamulo anu.
172 Lilime langa liimbe zokhudza mawu anu,+Chifukwa malamulo anu onse ndi olungama.
173 Dzanja lanu likhale lokonzeka kundithandiza,+Chifukwa ndasankha kumvera malamulo anu.+
174 Ndikulakalaka chipulumutso chanu, inu Yehova,Ndipo ndimakonda kwambiri chilamulo chanu.+
175 Ndithandizeni kuti ndikhale ndi moyo kuti ndikutamandeni,+Zigamulo zanu zindithandize.
176 Ndasochera ngati nkhosa yotayika.+ Ndifunefuneni ine mtumiki wanu,Chifukwa sindinaiwale malamulo anu.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “amachita zinthu mokhulupirika.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “njira zanga zikanakhala zokhazikika.”
^ Kapena kuti, “Ndidzaphunzira.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Mugubuduze nʼkundichotsera.”
^ Kapena kuti, “Ine mtumiki wanu ndimaphunzira.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “njira za.”
^ Kapena kuti, “ndiphunzire.”
^ Kapena kuti, “ndichite manyazi.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndidzathamanga mʼnjira za.”
^ Kapena kuti, “Ndiyendetseni.”
^ Kapena kuti, “munauza.”
^ Kapena kuti, “mawu anu.”
^ Kapena kuti, “ndikudikirira.”
^ Kapena kuti, “mʼmalo otakasuka.”
^ Kapena kuti, “Ndipo ndidzaphunzira.”
^ Kapena kuti, “lonjezo limene.”
^ Kapena kuti, “Mawu amene munachititsa kuti ndiziwayembekezera.”
^ Kapena kuti, “Mʼnyumba imene ndimakhala monga mlendo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndafewetsa nkhope yanu kuti mundimwetulire.”
^ Kapena kuti, “mawu anu.”
^ Kapena kuti, “ndinkachimwa mosadziwa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “yauma ngati mafuta oundana.”
^ Kapena kuti, “Chifukwa ndikuyembekezera mawu anu.”
^ Kapena kuti, “Mogwirizana ndi mawu anu.”
^ Kapena kuti, “ine ndidzaphunzira.”
^ Kapena kuti, “Chifukwa ndikuyembekezera mawu anu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amakhudza mbali zonse.”
^ Kapena kuti, “Ndimaphunzira.”
^ Kapena kuti, “Chifukwa ndimaphunzira.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “nsembe zaufulu za pakamwa panga.”
^ Kapena kuti, “Nthawi zonse moyo wanga umakhala mʼdzanja langa.”
^ Kapena kuti, “ndi cholowa changa chamuyaya.”
^ Kapena kuti, “Chifukwa ndikuyembekezera mawu anu.”
^ Kapena kuti, “mogwirizana ndi mawu anu.”
^ Kapena kuti, “chiyembekezo changa chindichititse manyazi.”
^ Kapena kuti, “mawu.”
^ Kapena kuti, “woyenga bwino.”
^ Kapena kuti, “malamulo.”
^ Kapena kuti, “kuti ndipumire mʼmwamba.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndiwomboleni.”
^ Kapena kuti, “indimwetulire.”
^ Kapena kuti, “Chifukwa ndikuyembekezera mawu anu.”
^ Kapena kuti, “Ndimadzuka maulonda a usiku asanathe.”
^ Kapena kuti, “Kuti ndiphunzire.”
^ Kapena kuti, “khalidwe lonyansa.”
^ Kapena kuti, “Ndiweruzireni mlandu wanga.”
^ Kapena kuti, “mawu anu.”
^ Kapena kuti, “Kwa iwo palibe chopunthwitsa.”
^ Kapena kuti, “mogwirizana ndi mawu anu.”