Salimo 138:1-8
Salimo la Davide.
138 Ndidzakutamandani ndi mtima wanga wonse.+
Ndidzakuimbirani nyimbo zokutamandaniPamaso pa milungu ina.
2 Ndidzawerama nditayangʼana kukachisi wanu woyera,*+Ndipo ndidzatamanda dzina lanu+Chifukwa cha kukhulupirika kwanu ndiponso chikondi chanu chokhulupirika.
Chifukwa mwasonyeza kuti dzina lanu komanso malonjezo anu ndi apamwamba kuposa china chilichonse.*
3 Pa tsiku limene ine ndinaitana, inu munandiyankha.+Munandilimbitsa mtima komanso kundipatsa mphamvu.+
4 Mafumu onse apadziko lapansi adzakutamandani, inu Yehova,+Chifukwa adzakhala atamva malonjezo amene mwanena.
5 Iwo adzaimba zokhudza njira za Yehova,Chifukwa ulemerero wa Yehova ndi waukulu.+
6 Ngakhale kuti Yehova ali pamwamba, amaona wodzichepetsa,+Koma wonyada samuyandikira.+
7 Ngakhale nditakumana ndi mavuto, inu mudzandithandiza kuti ndikhalebe ndi moyo.+
Mumagwiritsa ntchito mphamvu zanu polimbana ndi adani anga omwe ndi okwiya.Dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.
8 Yehova adzakwaniritsa zolinga zimene ali nazo pa ine.
Inu Yehova, chikondi chanu chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.+Musasiye ntchito ya manja anu.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “kumalo anu opatulika.”
^ Mabaibulo ena amati, “Chifukwa inu mwakuza mawu anu pamwamba pa dzina lanu.”