Salimo 105:1-45

  • Zimene Yehova anachitira anthu ake posonyeza kuti ndi wokhulupirika

    • Mulungu amakumbukira pangano lake (8-10)

    • “Musakhudze odzozedwa anga” (15)

    • Mulungu anagwiritsa ntchito Yosefe amene anali kapolo (17-22)

    • Zozizwitsa zimene Mulungu anachita ku Iguputo (23-36)

    • Ulendo wa Aisiraeli wochoka ku Iguputo (37-39)

    • Mulungu anakumbukira zimene analonjeza Abulahamu (42)

105  Yamikani Yehova,+ itanani pa dzina lake,Dziwitsani mitundu ya anthu ntchito zake.+  2  Muimbireni, muimbireni nyimbo zomutamanda,Ganizirani mozama* ntchito zake zonse zodabwitsa.+  3  Nyadirani dzina lake loyera.+ Mitima ya anthu ofunafuna Yehova isangalale.+  4  Funafunani Yehova+ ndipo muzidalira mphamvu zake. Nthawi zonse muzimupempha kuti akuthandizeni.*  5  Kumbukirani ntchito zodabwitsa zimene wachita,Kumbukirani zozizwitsa zake ndi ziweruzo zimene wapereka,+  6  Inu mbadwa* za Abulahamu mtumiki wake,+Inu ana a Yakobo, osankhidwa ake.+  7  Iye ndi Yehova Mulungu wathu.+ Ziweruzo zake zili padziko lonse lapansi.+  8  Amakumbukira pangano lake mpaka kalekale,+Lonjezo limene anapereka* ku mibadwo 1,000.+  9  Wakumbukira pangano limene anapangana ndi Abulahamu,+Komanso lumbiro limene analumbira kwa Isaki,+ 10  Limene analikhazikitsa monga lamulo kwa Yakobo,Komanso monga pangano lokhalapo mpaka kalekale kwa Isiraeli, 11  Pamene anati, “Ndidzakupatsa dziko la Kanani+Kuti likhale cholowa chako.”+ 12  Pamene ananena zimenezi, nʼkuti iwo ali ochepa.+Nʼkuti ali ochepa kwambiri komanso ali alendo mʼdzikolo.+ 13  Iwo ankayendayenda kuchokera ku mtundu wina kupita ku mtundu wina,Komanso kuchokera mu ufumu wina kupita kwa anthu a mtundu wina.+ 14  Mulungu sanalole kuti munthu aliyense awapondereze,+Koma anadzudzula mafumu chifukwa cha iwo.+ 15  Iye anati: “Musakhudze odzozedwa anga,Ndipo aneneri anga musawachitire choipa chilichonse.”+ 16  Iye anagwetsa njala yaikulu mʼdzikomo,+Iye anachititsa kuti asathenso kupeza chakudya.* 17  Mulungu anatsogoza Yosefe,Munthu amene anagulitsidwa kuti akhale kapolo.+ 18  Kumeneko anamanga* mapazi ake mʼmatangadza,+Khosi lake analiika mʼzitsulo 19  Mpaka nthawi imene zimene Mulungu ananena zinakwaniritsidwa,+Mawu a Yehova ndi amene anamuyenga. 20  Mfumu inalamula kuti amutulutse mʼndende,+Wolamulira mitundu ya anthu anatulutsa Yosefe mʼndende. 21  Anamupatsa udindo woyangʼanira banja lakeKomanso woyangʼanira chuma chake chonse.+ 22  Anamupatsa mphamvu zolamulira* akalonga ake mmene akufuniraKomanso kuti akuluakulu aziwaphunzitsa zinthu za nzeru.+ 23  Kenako Isiraeli anapita ku Iguputo+Ndipo Yakobo anakhala monga mlendo mʼdziko la Hamu. 24  Mulungu anachititsa kuti anthu ake aberekane kwambiri,+Iye anawachititsa kuti akhale amphamvu kwambiri kuposa adani awo.+ 25  Analola adaniwo kuti asinthe mitima yawo nʼkuyamba kudana ndi anthu ake,Komanso kukonzera chiwembu atumiki akewo.+ 26  Ndiyeno anatumiza Mose mtumiki wake,+Ndi Aroni+ amene anamusankha. 27  Iwowa anachita zizindikiro za Mulungu pamaso pa Aiguputo,Anachita zodabwitsa zake mʼdziko la Hamu.+ 28  Mulungu anachititsa kuti mʼdziko la Iguputo mukhale mdima.+Iwo* sanapandukire mawu ake. 29  Anasandutsa madzi a Aiguputo kukhala magazi,Ndipo anapha nsomba zawo.+ 30  Mʼdziko lawo munadzaza achule,+Ngakhalenso mʼzipinda za mafumu awo. 31  Analamula kuti pagwe ntchentche zoluma,Komanso tizilombo touluka toyamwa magazi,* mʼmadera awo onse.+ 32  Anawagwetsera matalala mʼmalo mwa mvula,Anagwetsa mphezi* mʼdziko lawo.+ 33  Anawononga mitengo yawo ya mpesa ndi ya mkuyuNdipo anakhadzula mitengo mʼdziko lawo. 34  Analamula kuti pagwe dzombe,Dzombe lingʼonolingʼono losawerengeka.+ 35  Dzombelo linadya zomera zonse mʼdziko lawo,Linadyanso mbewu zonse zamʼmunda mwawo. 36  Kenako Mulungu anapha mwana aliyense woyamba kubadwa mʼdziko lawo,+Chiyambi cha mphamvu zawo zobereka. 37  Anatulutsa anthu ake atatenga siliva ndi golide.+Ndipo pakati pa mafuko ake panalibe amene anapunthwa panjira. 38  Aiguputo anasangalala Aisiraeli atatuluka mʼdzikolo,Chifukwa ankawaopa kwambiri.+ 39  Mulungu anatumiza mtambo kuti uwateteze+ Komanso moto kuti uziwaunikira usiku.+ 40  Anapempha nyama ndipo anawapatsa zinziri,+Ankawadyetsa chakudya chochokera kumwamba.+ 41  Anatsegula thanthwe ndipo panatuluka madzi ambiri.+Madziwo anayenda ngati mtsinje kudutsa mʼchipululu.+ 42  Chifukwa iye anakumbukira lonjezo lake loyera limene analonjeza mtumiki wake Abulahamu.+ 43  Choncho Mulungu anatulutsa anthu ake mʼdzikomo anthuwo akusangalala,+Anatulutsa osankhidwa ake akufuula mokondwera. 44  Anawapatsa mayiko a anthu a mitundu ina,+Anatenga zinthu zimene mitundu ina ya anthu inapeza itagwira ntchito mwakhama,+ 45  Anachita zimenezi kuti asunge malangizo ake,+Komanso kusunga malamulo ake. Tamandani Ya!*

Mawu a M'munsi

^ Mabaibulo ena amati, “Nenani zokhudza.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Nthawi zonse muzifunafuna nkhope yake.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Lamulo limene anapereka.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Anathyola ndodo zonse zopachikapo mkate.” Nʼkutheka kuti izi ndi ndodo zimene ankazigwiritsa ntchito posunga mkate.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “anazunza.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “zomanga.”
^ Nʼkutheka kuti akunena Mose ndi Aroni.
^ Timeneti ndi tizilombo tingʼonotingʼono ta ku Iguputo timene timaluma ngati udzudzu.
^ Kapena kuti, “malawi a moto.”
^ Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.