Salimo 69:1-36

  • Pemphero lopempha kupulumutsidwa

    • “Kudzipereka kwanga panyumba yanu kuli ngati moto umene ukuyaka mumtima mwanga” (9)

    • “Ndiyankheni mwamsanga” (17)

    • “Anandipatsa vinyo wosasa kuti ndimwe” (21)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira kaimbidwe ka “Nyimbo ya Maluwa.” Salimo la Davide. 69  Ndipulumutseni, inu Mulungu, chifukwa madzi atsala pangʼono kutenga moyo wanga.+  2  Ndamira mʼmatope akuya, mmene mulibe malo oponda.+ Ndalowa mʼmadzi akuya,Ndipo mtsinje wa madzi othamanga wandikokolola.+  3  Ndatopa ndi kuitana,+Mawu anga asasa. Maso anga achita mdima poyembekezera Mulungu wanga.+  4  Anthu amene amadana nane popanda chifukwa+Ndi ambiri kuposa tsitsi lamʼmutu mwanga. Amene akufuna kuchotsa moyo wanga,Adani anga,* omwe ndi anthu achinyengo, achuluka kwambiri. Anandikakamiza kuti ndibweze zinthu zimene sindinabe.  5  Inu Mulungu, mukudziwa kupusa kwanga,Ndipo zolakwa zanga sizinabisike kwa inu.  6  Anthu onse amene akuyembekezera inu asachite manyazi chifukwa cha ine,Inu Ambuye Wamkulu Koposa, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. Anthu amene akufunafuna inu, asachite manyazi chifukwa cha ine,Inu Mulungu wa Isiraeli.  7  Ine ndanyozedwa chifukwa cha inu,+Manyazi aphimba nkhope yanga.+  8  Ndakhala mlendo kwa abale anga,Ndakhala mlendo pakati pa ana aamuna a mayi anga.+  9  Kudzipereka kwanga panyumba yanu kuli ngati moto umene ukuyaka mumtima mwanga,+Ndipo chipongwe cha anthu amene amakunyozani chandigwera.+ 10  Nditasonyeza kudzichepetsa posala kudya,*Anthu anandinyoza chifukwa cha zimenezo. 11  Pamene ndinavala ziguduli,Iwo anayamba kundinyoza.* 12  Anthu amene amakhala pageti la mzinda amandinena,Ndipo anthu oledzera amanena za ine akamaimba nyimbo zawo. 13  Ndidzapemphera kwa inu Yehova,Pa nthawi yovomerezeka kwa inu.+ Chifukwa cha chikondi chanu chokhulupirika chomwe ndi chochuluka, inu Mulungu,Ndiyankheni ndipo musonyeze kuti ndinu Mpulumutsi wanga wodalirika.+ 14  Ndipulumutseni mʼmatopeMusalole kuti ndimire. Ndipulumutseni kwa anthu amene amadana naneNdiponso ku madzi akuya.+ 15  Musalole kuti madzi osefukira andikokolole,+Kapena kuti ndimire mʼmadzi akuya,Kapenanso kuti dzenje* lindimeze nʼkutseka pakamwa pake.+ 16  Ndiyankheni inu Yehova, chifukwa chikondi chanu chokhulupirika ndi chabwino.+ Maso anu akhale pa ine, mogwirizana ndi chifundo chanu chomwe ndi chochuluka,+ 17  Ndipo musabise nkhope yanu kwa mtumiki wanu.+ Ndiyankheni mwamsanga, chifukwa ndili pamavuto aakulu.+ 18  Bwerani pafupi ndi ine ndipo mundipulumutse.Ndipulumutseni* kwa adani anga. 19  Inu mukudziwa mmene andinyozera, chipongwe chimene andichitira komanso mmene andichititsira manyazi.+ Adani anga onse mukuwaona. 20  Mtima wanga wasweka chifukwa cha kunyozedwa, ndipo bala lake ndi losachiritsika.* Ndimayembekezera kuti wina andimvera chisoni, koma panalibe ndi mmodzi yemwe,+Ndimayembekezera kuti wina anditonthoza, koma sanapezeke ngakhale mmodzi.+ 21  Koma mʼmalo mwa chakudya anandipatsa poizoni,*+Ndipo pamene ndinali ndi ludzu anandipatsa vinyo wosasa kuti ndimwe.+ 22  Tebulo lawo likhale msampha kwa iwo,Ndipo zinthu zimene zikuwayendera bwino zikhale ngati khwekhwe kwa iwo.+ 23  Maso awo achite mdima kuti asaone,Ndipo chititsani miyendo yawo kuti izinjenjemera* nthawi zonse. 24  Akhuthulireni ukali wanu,Ndipo mkwiyo wanu woyaka moto uwagwere.+ 25  Msasa wawo* ukhale bwinja,Ndipo mʼmatenti awo musapezeke munthu wokhalamo.+ 26  Chifukwa iwo amalondalonda munthu amene inu mwamulanga,Ndipo amakamba miseche ya ululu wa anthu amene inu mwawavulaza. 27  Muwapatse chilango champhamvu chifukwa cha zolakwa zawo,Ndipo asapindule ndi chilungamo chanu. 28  Mayina awo afufutidwe mʼbuku la anthu amoyo,*+Ndipo iwo asalembedwe mʼbuku limene muli mayina a anthu olungama.+ 29  Koma ine ndavutika ndipo ndikumva ululu.+ Inu Mulungu, mundipulumutse komanso munditeteze. 30  Ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina la Mulungu,Ndipo ndidzamulemekeza komanso kumuyamikira. 31  Zimenezi zidzasangalatsa kwambiri Yehova kuposa ngʼombe yamphongo,Kuposa ngʼombe yamphongo yaingʼono imene ili ndi nyanga komanso ziboda.+ 32  Anthu ofatsa adzaona zimenezi ndipo adzasangalala. Inu amene mukutumikira Mulungu, mitima yanu ipezenso mphamvu. 33  Chifukwa Yehova akumvetsera osauka,+Ndipo sadzanyoza anthu ake amene agwidwa ukapolo.+ 34  Kumwamba ndi dziko lapansi zimutamande,+Chimodzimodzinso nyanja ndi chilichonse choyenda mmenemo. 35  Chifukwa Mulungu adzapulumutsa Ziyoni,+Ndipo adzamanganso mizinda ya Yuda,Iwo adzakhala mmenemo nʼkulitenga* kuti likhale lawo. 36  Mbadwa za atumiki ake zidzatenga dzikolo kuti likhale cholowa chawo,+Ndipo anthu amene amakonda dzina lake+ adzakhala mmenemo.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Amene amandida popanda chifukwa.”
Mabaibulo ena amati, “Nditalira komanso kusala kudya.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndinakhala mwambi.”
Zikuoneka kuti “dzenje” limeneli ndi manda.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndiwomboleni.”
Kapena kuti, “ndipo ndafika potaya mtima.”
Kapena kuti, “chomera chapoizoni.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ziuno zawo kuti zizinjenjemera.”
Kapena kuti, “Msasa wawo wokhala ndi mpanda.”
Kapena kuti, “mʼbuku la moyo.”
Apa akunena dzikolo.