Salimo 84:1-12
Kwa wotsogolera nyimbo, pa Gititi.* Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+
84 Inu Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,Ine ndimakonda kwambiri chihema chanu chachikulu!+
2 Moyo wanga ukulakalaka kwambiri,Inde, ndafookeratu chifukwa cholakalakaMabwalo a Yehova.+
Mtima wanga ndi thupi langa zikufuula mosangalala kwa Mulungu wamoyo.
3 Ngakhale mbalame zapeza malo okhala kumenekoNdipo namzeze wadzimangira chisa chake,Mmene amasamaliramo ana akePafupi ndi guwa lanu lansembe lalikulu, inu Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,Mfumu yanga ndi Mulungu wanga!
4 Osangalala ndi anthu amene akukhala mʼnyumba yanu!+
Iwo akupitiriza kukutamandani.+ (Selah)
5 Osangalala ndi anthu amene amapeza mphamvu kuchokera kwa inu,+Amene mitima yawo imalakalaka misewu yaikulu yopita kunyumba yanu.
6 Akamadutsa mʼchigwa cha Baka,*Amasandutsa chigwacho kukhala malo opezeka akasupe.Ndipo mvula yoyambirira imabweretsa madalitso mʼchigwacho.
7 Mphamvu zawo zidzapitiriza kuwonjezeka pamene akuyenda.+Aliyense wa iwo amaonekera pamaso pa Mulungu mu Ziyoni.
8 Inu Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, imvani pemphero langa.Mvetserani, inu Mulungu wa Yakobo. (Selah)
9 Inu Mulungu wathu komanso chishango chathu,+ onani,*Yangʼanani nkhope ya wodzozedwa wanu.+
10 Kukhala tsiku limodzi mʼmabwalo anu nʼkwabwino kuposa kukhala kwinakwake masiku 1,000!+
Ndasankha kuima pakhomo la nyumba ya Mulungu wangaKuposa kukhala mʼmatenti a anthu oipa.
11 Chifukwa Yehova Mulungu ndi dzuwa+ ndiponso chishango.+Iye amatikomera mtima nʼkutipatsa ulemerero.
Yehova sadzalephera kupereka chinthu chilichonse chabwinoKwa anthu amene amachita zinthu mokhulupirika.+
12 Inu Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,Wosangalala ndi munthu amene amakukhulupirirani.+
Mawu a M'munsi
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “mʼchigwa cha zitsamba za baka.”
^ Mabaibulo ena amati, “Yangʼanani chishango chathu, Inu Mulungu.”