Salimo 71:1-24

  • Achikulire amadalira Mulungu

    • Kudalira Mulungu kuyambira pa unyamata (5)

    • “Pa nthawi imene mphamvu zanga zatha” (9)

    • ‘Mulungu wakhala akundiphunzitsa kuyambira ndili mnyamata’ (17)

71  Inu Yehova, ine ndathawira kwa inu. Musalole kuti ndichite manyazi.+   Mundilanditse ndi kundipulumutsa chifukwa ndinu wolungama. Tcherani khutu lanu* kwa ine nʼkundipulumutsa.+   Mukhale thanthwe langa lachitetezoLoti ndizilowamo nthawi zonse. Lamulani kuti ndipulumutsidwe,Chifukwa inu ndinu thanthwe langa ndi malo anga achitetezo.+   Inu Mulungu wanga, ndipulumutseni mʼmanja mwa woipa,+Kuti ndisagwidwe ndi munthu wochita zinthu mopondereza komanso wopanda chilungamo.   Chifukwa chiyembekezo changa ndi inu Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.Ndakhala ndikudalira inu kuyambira ndili mnyamata.+   Ndakhala ndikudalira inu kuchokera tsiku limene ndinabadwa.Inu ndi amene munanditulutsa mʼmimba mwa mayi anga.+ Ndimakutamandani nthawi zonse.   Ndakhala ngati chinthu chodabwitsa kwa anthu ambiri,Koma inu ndinu malo anga othawirako olimba.   Mʼkamwa mwanga mwadzaza mawu otamanda inu.+Tsiku lonse ndimanena za ulemerero wanu.   Musanditaye pa nthawi imene ndakalamba.+Musandisiye pa nthawi imene mphamvu zanga zatha.+ 10  Adani anga amandinenera zoipa,Ndipo anthu amene akufuna kuchotsa moyo wanga, amandikonzera chiwembu,+ 11  Iwo akunena kuti: “Mulungu wamusiya. Muthamangitseni nʼkumugwira chifukwa palibe womupulumutsa.”+ 12  Inu Mulungu, musakhale kutali ndi ine. Inu Mulungu wanga, ndithandizeni mofulumira.+ 13  Anthu amene akudana naneAchititsidwe manyazi ndipo awonongedwe.+ Amene akufuna nditakumana ndi tsokaAgwidwe manyazi ndipo anyozeke.+ 14  Koma ine ndipitiriza kuyembekezera.Ndidzakutamandani mowirikiza kuposa kale. 15  Pakamwa panga padzanena za chilungamo chanu,+Tsiku lonse padzanena za ntchito za chipulumutso chanu,Ngakhale kuti nʼzochuluka ndipo sindingathe kuzimvetsa.*+ 16  Ndidzabwera nʼkudzanena za zinthu zamphamvu zimene mumachita,Inu Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.Ndidzanena za chilungamo chanu chokha basi. 17  Inu Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ndili mnyamata,+Ndipo mpaka pano ndikupitiriza kulengeza ntchito zanu zodabwitsa.+ 18  Ngakhale nditakalamba nʼkumera imvi, inu Mulungu musandisiye.+ Ndiloleni kuti ndiuze mʼbadwo wotsatira za mphamvu zanu*Komanso za nyonga zanu kwa onse obwera mʼtsogolo.+ 19  Chilungamo chanu, inu Mulungu chafika kumwamba.+Mwachita zinthu zazikulu,Inu Mulungu, ndi ndani angafanane nanu?+ 20  Ngakhale kuti mwachititsa kuti ndikumane ndi mavuto komanso masoka ambiri,+Bwezeretsani mphamvu zanga.Nditulutseni mʼdzenje lakuya.*+ 21  Chulukitsani ulemu wanga,Ndipo mundizungulire ndi chitetezo chanu nʼkundilimbikitsa. 22  Mukatero, ndidzakutamandani ndi choimbira cha zingweChifukwa cha kukhulupirika kwanu, inu Mulungu.+ Ndidzakuimbirani nyimbo zokutamandani ndi zeze,Inu Woyera wa Isiraeli. 23  Pakamwa panga padzafuula mosangalala pamene ndikuimba nyimbo zokutamandani,+Chifukwa mwapulumutsa moyo wanga.*+ 24  Lilime langa lidzalankhula* za chilungamo chanu tsiku lonse,+Chifukwa anthu amene akufuna kundiwononga adzachita manyazi ndiponso kunyozeka.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Weramani nʼkumvetsera.”
Kapena kuti, “kuziwerenga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “dzanja lanu.”
Kapena kuti, “mʼmadzi akuya.”
Kapena kuti, “mwaombola moyo wanga.”
Kapena kuti, “Ndidzaganizira mozama.”