Salimo 61:1-8
-
Mulungu ndi nsanja yolimba imene imateteza kwa adani
-
“Ndidzakhala mlendo mutenti yanu” (4)
-
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe ndi zoimbira za zingwe. Salimo la Davide.
61 Inu Mulungu, imvani kulira kwanga kopempha thandizo.
Mvetserani pemphero langa mwatcheru.+
2 Kuchokera kumalekezero a dziko lapansi ndidzafuulira inuPamene mtima wanga walefuka.*+
Nditsogolereni nʼkundikweza pathanthwe lalitali kuposa msinkhu wanga.+
3 Chifukwa inu ndinu malo anga othawirako,Nsanja yolimba imene imanditeteza kwa mdani.+
4 Ndidzakhala mlendo mutenti yanu mpaka kalekale.+Ndidzabisala mumthunzi wa mapiko anu.+ (Selah)
5 Chifukwa inu Mulungu, mwamva malonjezo anga.
Mwandipatsa cholowa chimene ndi cha anthu amene amaopa dzina lanu.+
6 Mudzatalikitsa moyo wa mfumu,*+Ndipo idzakhala ndi moyo ku mibadwomibadwo.
7 Mfumuyo idzakhala pampando wachifumu mpaka kalekale pamaso pa Mulungu.+Chikondi chanu chokhulupirika komanso kukhulupirika kwanu ziiteteze.+
8 Mukatero ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu mpaka kalekale,+Pamene ndikukwaniritsa malonjezo anga tsiku ndi tsiku.+