Salimo 146:1-10

  • Kudalira Mulungu, osati anthu

    • Munthu akafa zimene amaganiza zimatheratu (4)

    • Mulungu amadzutsa anthu amene awerama (8)

146  Tamandani Ya!*+ Moyo wanga wonse utamande Yehova.+   Ndidzatamanda Yehova kwa moyo wanga wonse. Ndidzaimbira Mulungu wanga nyimbo zomutamanda kwa moyo wanga wonse.   Musamakhulupirire anthu olemekezeka*Kapena mwana wa munthu amene sangabweretse chipulumutso.+   Mpweya* wake umachoka, ndipo iye amabwerera kunthaka.+Pa tsiku limenelo zonse zimene amaganiza zimatheratu.+   Wosangalala ndi munthu amene amathandizidwa ndi Mulungu wa Yakobo,+Amene chiyembekezo chake chili mwa Yehova Mulungu wake,+   Amene anapanga kumwamba komanso dziko lapansi,Nyanja ndiponso zonse zimene zili mmenemo,+Amene amakhala wokhulupirika nthawi zonse,+   Amene amaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa anthu amene achitiridwa chinyengo,Amene amapereka chakudya kwa anthu anjala.+ Yehova akumasula anthu amene ali mʼndende.*+   Yehova akutsegula maso a anthu amene ali ndi vuto losaona.+Yehova akudzutsa anthu amene awerama chifukwa cha mavuto.+Yehova amakonda anthu olungama.   Yehova akuteteza alendo amene akukhala mʼdziko la eni.Amathandiza mwana wamasiye komanso mkazi wamasiye.+Koma amasokoneza mapulani a anthu oipa.*+ 10  Yehova adzakhala Mfumu kwamuyaya,+Mulungu wako, iwe Ziyoni, adzakhala Mfumu ku mibadwomibadwo. Tamandani Ya!*

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
Kapena kuti, “Musamakhulupirire akalonga.”
Kapena kuti, “Mzimu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene amangidwa.”
Kapena kuti, “Koma amakhotetsa njira ya anthu oipa.”
Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.