Salimo 142:1-7
Masikili.* Salimo ndiponso pemphero la Davide, pamene anali kuphanga.+
142 Ndimafuulira Yehova kuti andithandize.+Ndimachonderera Yehova kuti andikomere mtima.
2 Ndimakhuthula nkhawa zanga pamaso pake.Ndimafotokoza mavuto anga pamaso pake+
3 Pamene mphamvu zanga zatha.*
Ndikatero, mumayangʼanitsitsa njira yanga.+
Adani anga anditchera msamphaMʼnjira imene ndikuyenda.
4 Yangʼanani kudzanja langa lamanja ndipo muoneKuti palibe aliyense amene akusamala za ine.*+
Palibenso kulikonse kumene ndingathawire,+Ndipo palibe amene akundidera nkhawa.
5 Ndikuitana inu Yehova kuti mundithandize.
Ndikunena kuti: “Inu ndinu malo anga othawirako,+Malo okhawo amene ndili nawo* mʼdziko la anthu amoyo.”
6 Mvetserani kulira kwanga kopempha thandizo,Chifukwa ndavutika kwambiri.
Ndipulumutseni kwa anthu amene akundizunza,+Chifukwa iwo ndi amphamvu kuposa ine.
7 Nditulutseni mundende yamdimaKuti nditamande dzina lanu.
Anthu olungama andizungulireChifukwa mumandichitira zabwino.
Mawu a M'munsi
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “Pamene mtima wanga walefuka.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “akuzindikira kuti ndilipo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Gawo langa.”