Salimo 26:1-12

  • Kuchita zinthu mokhulupirika

    • “Ndifufuzeni, Inu Yehova” (2)

    • Kupewa kugwirizana ndi anthu oipa (4, 5)

    • ‘Ndidzayenda mozungulira guwa lansembe la Mulungu’ (6)

Salimo la Davide. 26  Ndiweruzeni, inu Yehova, chifukwa ndimachita zinthu mokhulupirika.+Nthawi zonse ndimadalira inu Yehova.+   Ndifufuzeni, inu Yehova, ndipo mundiyese.Yengani maganizo anga* komanso mtima wanga.+   Chifukwa nthawi zonse ndimaganizira mozama za chikondi chanu chokhulupirika,Ndipo ndimayenda mʼchoonadi chanu.+   Sindicheza* ndi anthu achinyengo,+Ndipo ndimapewa anthu amene amabisa umunthu wawo.*   Ndimadana ndi zokhala pagulu la anthu ochita zoipa,+Ndipo ndimakana kucheza* ndi anthu oipa.+   Ndidzasamba mʼmanja mwanga kusonyeza kuti ndine wosalakwa,Ndipo ndidzayenda mozungulira guwa lanu lansembe, inu Yehova,   Kuti mawu anga oyamikira amveke,+Komanso kuti ndilengeze ntchito zanu zonse zodabwitsa.   Yehova, ndimakonda nyumba imene inu mumakhala,+Malo amene kumakhala ulemerero wanu.+   Musandiwononge limodzi ndi anthu ochimwa,+Kapena kuchotsa moyo wanga limodzi ndi anthu achiwawa.* 10  Amene manja awo amachita khalidwe lochititsa manyazi,Ndipo mʼdzanja lawo lamanja mwadzaza ziphuphu. 11  Koma ine, ndidzapitiriza kuchita zinthu mokhulupirika. Ndipulumutseni* ndipo mundikomere mtima. 12  Phazi langa laima pamalo otetezeka.+Ndidzatamanda Yehova mumpingo* waukulu.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mmene ndikumvera mumtima mwanga.” Mʼchilankhulo choyambirira, “impso zanga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Sindikhala pansi.”
Kapena kuti, “Sindichita zinthu limodzi ndi anthu achinyengo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kukhala pansi.”
Kapena kuti, “anthu a mlandu wa magazi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndiwomboleni.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pamsonkhano.”