Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

FUNSO 1

Kodi Mulungu Ndi Ndani?

“Anthu adziwe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, inu nokha ndinu Wamʼmwambamwamba, woyenera kulamulira dziko lonse lapansi.”

Salimo 83:18

“Dziwani kuti Yehova ndi Mulungu. Iye ndi amene anatipanga, ndipo ndife ake.”

Salimo 100:3

“Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli. Sindipereka ulemerero wanga kwa wina aliyense ndipo sindifuna kuti aliyense azitamanda zifaniziro zogoba mʼmalo mwa ine.”

Yesaya 42:8

“Aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.”

Aroma 10:13

“Nʼzoona kuti nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu.”

Aheberi 3:4

“Kwezani maso anu kumwamba ndipo muone. Kodi ndi ndani amene analenga zinthu zimenezi? Ndi amene akutsogolera gulu lonse la nyenyezi ndipo zonse amaziwerenga. Iliyonse amaiitana poitchula dzina lake. Chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zake zoopsa ndiponso chifukwa chakuti ali ndi mphamvu zambiri zochitira zinthu, palibe iliyonse imene imasowa.”

Yesaya 40:26