Salimo 15:1-5

  • Ndi ndani amene angakhale mlendo mutenti ya Yehova?

    • Amalankhula zoona mumtima mwake (2)

    • Iye sanena miseche (3)

    • Amakwaniritsa zimene analonjeza ngakhale kuti ndi zopweteka kwa iye (4)

Nyimbo ya Davide. 15  Inu Yehova, ndi ndani amene angakhale mlendo mutenti yanu? Ndi ndani amene angakhale mʼphiri lanu lopatulika?+   Ndi amene akuyenda mosalakwitsa zinthu,*+Amene amachita zinthu zabwino+Komanso kulankhula zoona mumtima mwake.+   Iye sanena miseche ndi lilime lake,+Sachitira mnzake choipa chilichonse,+Ndipo sanyoza* anzake.+   Iye sagwirizana ndi munthu aliyense wonyansa,+Koma amalemekeza anthu amene amaopa Yehova. Sasintha zimene walonjeza* ngakhale zinthu zitakhala kuti sizili bwino kwa iye.+   Sakongoza ndalama zake kuti alandire chiwongoladzanja,+Ndipo salandira chiphuphu kuti akhotetse mlandu wa munthu wosalakwa.+ Munthu aliyense amene amachita zimenezi, sadzagwedezeka.*+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mokhulupirika.”
Kapena kuti, “sachititsa manyazi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “lumbiro.”
Kapena kuti, “sadzayenda dzandidzandi.”