Salimo 140:1-13
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.
140 Inu Yehova, ndipulumutseni kwa anthu oipa.Nditetezeni kwa anthu ochita zachiwawa,+
2 Anthu amene amakonza chiwembu mʼmitima yawo+Ndipo amayambitsa mikangano tsiku lonse.
3 Anola lilime lawo ndipo lakhala ngati la njoka.+Mʼmilomo yawo muli poizoni wa mphiri.+ (Selah)
4 Inu Yehova, nditetezeni kuti manja a munthu woipa asandikhudze.+Nditetezeni kwa anthu amene amachita zachiwawa.Amene amakonza chiwembu kuti andivulaze.
5 Anthu onyada anditchera msampha.Iwo agwiritsa ntchito zingwe kuti atchere ukonde mʼmphepete mwa njira,+
Ndipo anditchera makhwekhwe.+ (Selah)
6 Ndauza Yehova kuti: “Inu ndinu Mulungu wanga.
Mvetserani inu Yehova, kuchonderera kwanga kopempha thandizo.”+
7 Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, Mpulumutsi wanga wamphamvu,Mwateteza mutu wanga pa tsiku lankhondo.+
8 Inu Yehova, musapatse anthu oipa zimene amalakalaka.
Musalole kuti ziwembu zawo zitheke kuti angayambe kunyada.+ (Selah)
9 Mitu ya anthu amene andizunguliraIphimbidwe ndi zoipa zimene amalankhula.+
10 Muwakhuthulire makala oyaka moto pamutu pawo.+
Aponyedwe pamoto,Mʼmaenje akuya*+ ndipo asadzukenso.
11 Munthu wonenera anzake zoipa asapeze malo padziko lapansi.*+
Zoipa zisakesake anthu ochita zachiwawa ndipo ziwawononge.
12 Ndikudziwa kuti Yehova adzateteza anthu onyozeka pa mlandu wawoNdipo adzachitira chilungamo anthu osauka.+
13 Ndithudi, anthu olungama adzatamanda dzina lanu.Anthu owongoka mtima adzakhala pamaso panu.+