Salimo 4:1-8

  • Pemphero losonyeza kuti tikudalira Mulungu

    • “Ngati mwakwiya, musachimwe” (4)

    • ‘Ndidzagona mwamtendere nʼkupeza tulo’ (8)

Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Nyimbo ya Davide. 4  Ndikaitana, mundiyankhe inu Mulungu wanga wolungama.+ Mundikonzere njira yoti ndipulumukire* mʼmasautso anga. Mundikomere mtima ndipo imvani pemphero langa.   Inu ana a anthu, kodi mudzandinyoza mʼmalo mondilemekeza mpaka liti? Kodi mudzakonda zinthu zopanda pake komanso kufufuza zinthu zoti mundinamizire mpaka liti? (Selah)   Dziwani kuti Yehova adzachita zinthu zapadera kwa munthu amene ndi wokhulupirika kwa iye.*Yehova adzamva ndikaitana.   Ngati mwakwiya, musachimwe.+ Lankhulani mumtima mwanu muli pabedi panu ndipo mukhale chete. (Selah)   Nsembe iliyonse imene mukupereka kwa Mulungu, muziipereka ndi mtima wabwino,Ndipo muzikhulupirira Yehova.+   Pali ambiri amene akunena kuti: “Ndi ndani amene adzationetse chinthu chabwino chilichonse?” Inu Yehova, kuwala kwa nkhope yanu kutiunikire.+   Mwadzaza mtima wanga ndi chisangalalo chachikuluKuposa amene ali ndi zokolola zochuluka komanso vinyo watsopano.   Ndidzagona pansi mwamtendere nʼkupeza tulo,+Chifukwa inu nokha Yehova mumandichititsa kukhala wotetezeka.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mundikonzere malo otakasuka.”
Kapena kuti, “adzasiyanitsa munthu wokhulupirika kwa iye; adzapatula munthu wokhulupirika kwa iye.”