Salimo 35:1-28
Salimo la Davide.
35 Inu Yehova, nditetezeni kwa anthu amene akundiimba mlandu.+Menyanani ndi anthu amene akumenyana ndi ine.+
2 Tengani chishango chanu chachingʼono ndi chachikulu,+Ndipo nyamukani ndi kunditeteza.+
3 Tengani mkondo ndi nkhwangwa yapankhondo kuti mulimbane ndi adani anga amene akundithamangitsa.+
Ndiuzeni kuti:* “Ine ndine chipulumutso chako.”+
4 Amene akufunafuna moyo wanga achite manyazi komanso anyozeke.+
Amene akukonza chiwembu choti andiphe abwerere mwamanyazi.
5 Akhale ngati mankhusu* ouluzika ndi mphepo,Mngelo wa Yehova awathamangitse.+
6 Njira yawo ikhale yamdima ndi yotereraPamene mngelo wa Yehova akuwathamangitsa.
7 Popanda chifukwa, iwo atchera ukonde kuti andikole.Akumba dzenje kuti ndigweremo ngakhale kuti sindinalakwe.
8 Tsoka liwagwere modzidzimutsa,Akodwe mu ukonde umene atchera okha.Agweremo nʼkufa.+
9 Koma ine ndidzakondwera chifukwa cha zimene Yehova wachita.Ndidzasangalala chifukwa wandipulumutsa.
10 Ndinena ndi mtima wanga wonse kuti:
“Inu Yehova, ndi ndani angafanane ndi inu?
Mumapulumutsa anthu ovutika mʼmanja mwa anthu amphamvu kuposa iwowo.+Mumapulumutsa anthu ovutika komanso anthu osauka kwa anthu amene akuwalanda zinthu zawo.”+
11 Mboni zoipa mtima zabwera,+Ndipo zikundifunsa zinthu zimene sindikuzidziwa.
12 Iwo amandibwezera zoipa mʼmalo mwa zabwino,+Ndipo ndimakhala wachisoni ngati namfedwa.
13 Koma akadwala ndinkavala chiguduli,Ndinkasala kudya posonyeza kudzichepetsa.Ndipo pemphero langa likapanda kuyankhidwa,
14 Ndinkayendayenda ndikulira ngati kuti ndikulira maliro a mnzanga kapena mchimwene wanga,Ndinkawerama chifukwa cha chisoni ngati munthu amene akulira maliro a mayi ake.
15 Koma nditapunthwa anasangalala ndipo anasonkhana pamodzi.Anasonkhana pamodzi kuti andibisalire nʼkundiukira.Anandikhadzulakhadzula ndipo sanakhale chete.
16 Anthu osaopa Mulungu akundinyoza mwachipongwe,Iwo akundikukutira mano.+
17 Inu Yehova, kodi mudzayangʼanira zimenezi mpaka liti?+
Ndipulumutseni kuti asandiphe,+Pulumutsani moyo wanga,* womwe ndi wamtengo wapatali, kwa mikango yamphamvu.*+
18 Mukatero, ndidzakuyamikirani mumpingo waukulu.+Ndidzakutamandani pakati pa anthu ambiri.
19 Musalole kuti anthu amene amadana nane popanda chifukwa+ asangalale chifukwa cha mavuto anga.Musalole kuti anthu amene amadana nane popanda chifukwa andipsinyire diso mondinyoza.+
20 Chifukwa iwo salankhula mwamtendere,Koma mwachinyengo, amakonzera chiwembu anthu okonda mtendere amʼdzikoli.+
21 Iwo amatsegula kwambiri pakamwa pawo kuti atsutsane nane,Iwo amati: “Eya! Eya! Taona tokha ndi maso athuwa.”
22 Inu Yehova, mwaona zimenezi. Choncho musakhale chete.+
Inu Yehova, musakhale kutali ndi ine.+
23 Khalani tcheru ndipo nyamukani ndi kunditeteza,Inu Mulungu wanga Yehova, nditetezeni pa mlandu wanga.
24 Inu Yehova Mulungu wanga, mundiweruze mogwirizana ndi mfundo zanu zolungama,+Musalole kuti adani anga asangalale chifukwa cha mavuto anga.
25 Musalole kuti mumtima mwawo anene kuti: “Eya! Tapeza zimene timafuna.”
Ndipo asanene kuti: “Tamumeza.”+
26 Onsewo achite manyazi nʼkuthedwa nzeru,Onse amene amasangalala tsoka likandigwera.
Onse amene amadzikweza pamaso panga atsitsidwe ndipo achite manyazi.
27 Koma amene amakonda chilungamo changa afuule mosangalala.Nthawi zonse azinena kuti:
“Alemekezeke Yehova, amene amasangalala mtumiki wake akakhala pamtendere.”+
28 Ndipo lilime langa lidzafotokoza* za chilungamo chanu,+Komanso kukutamandani tsiku lonse.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Uzani moyo wanga kuti.”
^ “Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa popuntha mbewu ngati mpunga ndipo amatha kuuluzika ndi mphepo.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “wanga wokhawu,” kutanthauza moyo wake.
^ Kapena kuti, “mikango yamphamvu yamanyenje.”
^ Kapena kuti, “lidzaganizira mozama.”