Salimo 75:1-10
-
Mulungu amaweruza mwachilungamo
-
Anthu oipa adzamwa zamʼkapu ya Yehova (8)
-
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira kaimbidwe ka nyimbo yakuti “Musandiwononge.” Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+
75 Timakuyamikani, inu Mulungu, timakuyamikani.Dzina lanu lili pafupi ndi ife,+Ndipo anthu akulengeza ntchito zanu zodabwitsa.
2 Inu mukuti: “Ndikasankha nthawi yoti ndiweruze,Ndimaweruza mwachilungamo.
3 Pamene dziko lapansi ndi onse okhala mmenemo ananjenjemera* ndi mantha,Ine ndi amene ndinalimbitsa zipilala zake.” (Selah)
4 Anthu odzitukumula ndinawauza kuti, “Musadzitukumule,”
Ndipo oipa ndinawauza kuti, “Musadzikuze chifukwa choti muli ndi mphamvu.*
5 Musadzikuze chifukwa choti muli ndi mphamvu*Kapena kulankhula mwamatama.
6 Chifukwa ulemu wa munthu suchokeraKumʼmawa, kumadzulo kapena kumʼmwera.
7 Mulungu ndiye woweruza.+
Amatsitsa munthu wina nʼkukweza wina.+
8 Mʼdzanja la Yehova muli kapu.+Vinyo akuchita thovu ndipo wasakanizidwa bwino.
Ndithudi, iye adzakhuthula vinyo yenseNdipo anthu onse oipa padziko lapansi adzamwa mpaka kugugudiza nsenga zake.”+
9 Koma ine ndidzalengeza zimenezi mpaka kalekale.Ndidzaimba nyimbo zotamanda Mulungu wa Yakobo.
10 Mulungu akuti: “Ndidzathetsa mphamvu* zonse za anthu oipa,Koma ndidzachititsa kuti mphamvu* za anthu olungama zionekere bwino.”
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “anasungunuka.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Musakweze nyanga yanu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Musakweze nyanga yanu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “nyanga.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “nyanga.”