Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

FUNSO 19

Kodi Mʼmabuku a MʼBaibulo Muli Zotani?

MALEMBA A CHIHEBERI (“CHIPANGANO CHAKALE”)

MABUKU 5 OYAMBIRIRA:

Genesis, Ekisodo, Levitiko, Numeri ndi Deuteronomo

Zimene zinachitika kuyambira nthawi imene zinthu zinalengedwa mpaka kuyamba kwa mtundu wa Isiraeli

MABUKU 12 OFOTOKOZA MBIRI YA AISIRAELI:

Yoswa, Oweruza ndi Rute

Zimene zinachitika Aisiraeli akulowa mʼDziko Lolonjezedwa ndiponso atalowa

1 ndi 2 Samueli, 1 ndi 2 Mafumu, 1 ndi 2 Mbiri

Mbiri ya Aisiraeli mpaka pamene Yerusalemu anawonongedwa

Ezara, Nehemiya ndi Esitere

Mbiri ya Ayuda atabwerera kuchoka ku ukapolo ku Babulo

MABUKU 5 ANDAKATULO:

Yobu, Masalimo, Miyambo, Mlaliki ndi Nyimbo ya Solomo

Mʼmabuku amenewa muli mawu anzeru komanso nyimbo

MABUKU 17 AMAULOSI:

Yesaya, Yeremiya, Maliro, Ezekieli, Danieli, Hoseya, Yoweli, Amosi, Obadiya, Yona, Mika, Nahumu, Habakuku, Zefaniya, Hagai, Zekariya ndi Malaki

Maulosi okhudza anthu a Mulungu

MALEMBA A CHIGIRIKI (“CHIPANGANO CHATSOPANO”)

MABUKU 4 A UTHENGA WABWINO:

Mateyu, Maliko, Luka ndi Yohane

Mbiri ya moyo wa Yesu komanso utumiki wake

BUKU LA MACHITIDWE A ATUMWI:

Mmene mpingo wa Chikhristu unayambira komanso ntchito ya umishonale

MAKALATA 21:

Aroma, 1 ndi 2 Akorinto, Agalatiya, Aefeso, Afilipi, Akolose, 1 ndi 2 Atesalonika

Makalata opita kumipingo yosiyanasiyana

1 ndi 2 Timoteyo, Tito ndi Filimoni

Makalata opita kwa Akhristu odziwika ndi dzina la bukulo

Aheberi, Yakobo, 1 ndi 2 Petulo, 1, 2 ndi 3 Yohane komanso Yuda

Makalata opita kwa Akhristu osiyanasiyana

BUKU LA CHIVUMBULUTSO:

Masomphenya osiyanasiyana amene mtumwi Yohane anaonetsedwa