Salimo 58:1-11

  • Pali Mulungu amene amaweruza dziko lapansi

    • Pemphero lopempha kuti anthu oipa alangidwe (6-8)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira kaimbidwe ka nyimbo yakuti “Musandiwononge.” Salimo la Davide. Mikitamu.* 58  Kodi mungalankhule bwanji za chilungamo mutakhala chete?+ Kodi mungaweruze mwachilungamo, inu ana a anthu?+  2  Ayi, mʼmalomwake mukuganiza zochita zinthu zopanda chilungamo mumtima mwanu,+Ndipo mumalimbikitsa zachiwawa mʼdzikoli.+  3  Oipa amasochera* akangobadwa.*Iwo amakhala osamvera komanso abodza kuchokera nthawi imene anabadwa.  4  Iwo ali ndi poizoni ngati wa njoka.+Ndipo ndi ogontha ngati njoka ya mamba imene yatseka makutu ake.  5  Singamve mawu a anthu amatsenga,Ngakhale atachita matsengawo mwaluso.  6  Inu Mulungu, agululeni mano mʼkamwa mwawo. Inu Yehova, thyolani nsagwada za mikango* imeneyi.  7  Asowe ngati madzi amene akuyenda. Mulungu akoke uta wake nʼkuwagwetsa ndi mivi yake.  8  Akhale ngati nkhono imene imasungunuka ikamayenda.Ngati mwana wa mayi amene wapita padera, yemwe saona dzuwa.  9  Miphika yanu isanayambe kumva kutentha kwa moto wa mitengo yaminga,Mulungu adzauluza mitengo yaiwisi komanso imene ikuyaka ngati ikuuluzika ndi mphepo yamkuntho.+ 10  Wolungama adzasangalala chifukwa chakuti waona oipa akupatsidwa chilango.+Mapazi ake adzaponda magazi a anthu oipa.+ 11  Kenako anthu adzati: “Ndithudi wolungama amalandira mphoto.+ Ndithudi pali Mulungu amene amaweruza padziko lapansi.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “amachita zoipa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kuchokera mʼmimba.”
Kapena kuti, “mikango yamphamvu yamanyenje.”