Salimo 92:1-15

  • Yehova ndi wokwezeka mpaka kalekale

    • Ntchito zake ndi zazikulu komanso maganizo ake ndi ozama kwambiri (5)

    • ‘Olungama zinthu zidzawayendera bwino ngati mtengo’ (12)

    • Okalamba zinthu zidzapitirizabe kuwayendera bwino (14)

Nyimbo ndi Salimo la pa tsiku la Sabata. 92  Ndi bwino kuyamika inu Yehova,+Ndiponso kuimba nyimbo zotamanda dzina lanu, inu Wamʼmwambamwamba.   Ndi bwino kulengeza chikondi chanu chokhulupirika+ mʼmawa,Ndi kukhulupirika kwanu usiku,   Pogwiritsa ntchito choimbira cha zingwe 10 ndi choimbira cha zingwe zitatu,Komanso nyimbo zosangalatsa zoimbidwa ndi zeze.+   Inu Yehova mwachititsa kuti ndisangalale chifukwa cha zochita zanu.Ndimafuula mosangalala chifukwa cha ntchito za manja anu.   Ntchito zanu ndi zazikulu kwambiri inu Yehova!+ Maganizo anu ndi ozama kwambiri.+   Munthu wopanda nzeru sangadziwe zimenezi,Ndipo munthu wopusa sangamvetse izi:+   Anthu oipa akaphuka ngati msipuNdipo anthu onse ochita zoipa zinthu zikamawayendera bwino,Zimatero kuti awonongedwe kwamuyaya.+   Koma inu Yehova, ndinu wokwezeka mpaka kalekale.   Onani adani anu atagonjetsedwa, inu Yehova,Onani mmene adani anu adzathere,Onse ochita zoipa adzamwazikana.+ 10  Koma inu mudzawonjezera mphamvu* zanga kuti zikhale ngati za ngʼombe yamphongo yamʼtchire.Khungu langa ndidzalidzoza mafuta abwino kwambiri.+ 11  Maso anga adzaona adani anga atagonja.+Makutu anga adzamva za kugwa kwa anthu oipa amene amandiukira. 12  Koma olungama zinthu zidzawayendera bwino ngati mtengo wa kanjedzaNdipo adzakula kwambiri ngati mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni.+ 13  Iwo anadzalidwa mʼnyumba ya Yehova,Zinthu zikuwayendera bwino mʼmabwalo a Mulungu wathu.+ 14  Ngakhale atakalamba* zinthu zidzapitirizabe kuwayendera bwino.+Adzakhalabe amphamvu* ndi athanzi,+ 15  Ndipo adzalengeza kuti Yehova ndi wolungama. Iye ndi Thanthwe langa,+ ndipo sachita zosalungama.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “nyanga.”
Kapena kuti, “atachita imvi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “onenepa.”