Salimo 68:1-35

  • ‘Adani a Mulungu amwazikeʼ

    • “Bambo wa ana amasiye” (5)

    • Mulungu amapereka nyumba kwa anthu amene alibe wowathandiza (6)

    • Akazi amene akulengeza uthenga wabwino (11)

    • Mphatso za amuna (18)

    • ‘Yehova amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku’ (19)

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo ndi nyimbo ya Davide. 68  Mulungu anyamuke, adani ake amwazike,Ndipo amene amadana naye athawe pamaso pake.+  2  Mofanana ndi mphepo imene imathamangitsa utsi, inunso muwathamangitsire kutali.Mofanana ndi phula limene limasungunuka pamoto,Anthu oipa awonongeke pamaso pa Mulungu.+  3  Koma olungama asangalale,+Asangalale kwambiri pamaso pa Mulungu,Adumphe ndi chisangalalo.  4  Imbirani Mulungu, muimbireni nyimbo zotamanda dzina lake.+ Imbirani Iye amene akudutsa mʼchipululu.* Dzina lake ndi Ya.*+ Sangalalani pamaso pake.  5  Bambo wa ana amasiye komanso amene amateteza* akazi amasiye+Ndi Mulungu amene amakhala mʼmalo ake oyera.+  6  Anthu amene alibe wowathandiza, Mulungu amawapatsa nyumba kuti azikhalamo.+Amamasula akaidi nʼkuwathandiza kuti zinthu ziwayendere bwino.+ Koma anthu osamvera* adzakhala mʼdziko louma.+  7  Inu Mulungu, pamene munkatsogolera anthu anu,+Pamene munkadutsa mʼchipululu, (Selah)  8  Dziko lapansi linagwedezeka,+Kumwamba kunagwa mvula chifukwa cha inu Mulungu,Phiri la Sinai ili linagwedezeka chifukwa cha inu Mulungu, Mulungu wa Isiraeli.+  9  Inu Mulungu, munagwetsa mvula yokwanira.Munapatsa mphamvu anthu anu amene anali ofooka.* 10  Iwo ankakhala mʼmudzi wanu wamatenti.+Inu Mulungu, chifukwa chakuti ndinu wabwino, munapereka zinthu zofunika kwa anthu osauka. 11  Yehova wapereka lamulo* kwa anthu ake,Ndipo akazi amene akulengeza uthenga wabwino* ndi gulu lalikulu.+ 12  Mafumu okhala ndi magulu a asilikali amathawa,+ ndithu amathawadi. Mkazi amene amangokhala pakhomo, amalandira nawo zinthu zimene zalandidwa kunkhondo.+ 13  Ngakhale anthu inu mutagona pambali pa moto mumsasa,Mudzalandira njiwa imene mapiko ake ndi okutidwa ndi siliva,Ndipo nthenga zakumapeto a mapiko ake ndi zagolide woyenga bwino.* 14  Pamene Wamphamvuyonse anamwaza mafumu amʼdzikomo,+Mu Zalimoni munagwa sinowo.* 15  Phiri la ku Basana+ ndi phiri la Mulungu.*Phiri la ku Basana ndi phiri lansonga zitalizitali. 16  Nʼchifukwa chiyani inu mapiri ansonga zitalizitali mumayangʼana mwansanjePhiri limene Mulungu wasankha* kuti azikhalamo?+ Ndithudi, Yehova adzakhala mʼphiri limenelo mpaka kalekale.+ 17  Magaleta ankhondo a Mulungu ali mʼmagulu a masauzande osawerengeka, ali mʼmagulu masauzandemasauzande.+ Yehova walowa mʼmalo oyera kuchokera kuphiri la Sinai.+ 18  Munakwera pamalo apamwamba.+Munatenga anthu ogwidwa ukapolo.Munatenga amuna kuti akhale mphatso,+Ndithu inu Ya,* Mulungu wathu, mwatenga ngakhale anthu osamvera+ kuti mukhale pakati pawo. 19  Atamandike Yehova, amene amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku,+Mulungu woona amene amatipulumutsa. (Selah) 20  Mulungu woona ndi Mulungu amene amatipulumutsa.+Ndipo Yehova Ambuye Wamkulu Koposa amatipulumutsa ku imfa.+ 21  Ndithudi, Mulungu adzaphwanya mitu ya adani ake,Adzaphwanya mutu wa aliyense amene akupitiriza* kuchita machimo.+ 22  Yehova wanena kuti: “Ndidzawabweza kuchokera ku Basana,+Ndidzawatulutsa mʼnyanja yakuya, 23  Kuti mapazi anu aponde magazi a adani anu,+Ndiponso kuti malilime a agalu anu anyambite magazi a adani anu.” 24  Iwo aona magulu a anthu anu akuyendera pamodzi, inu Mulungu,Magulu a anthu oyendera pamodzi a Mulungu wanga, Mfumu yanga, akulowa kumalo opatulika.+ 25  Oimba nyimbo akuyenda patsogolo, oimba zoimbira za zingwe akuyenda pambuyo pawo,+Pakati pali atsikana amene akuimba maseche.+ 26  Pamisonkhano tamandani Mulungu,Tamandani Yehova, inu nonse amene moyo wanu ukuchokera mu Kasupe wa Isiraeli.+ 27  Pali fuko lalingʼono la Benjamini+ limene likugonjetsa anthu,Pali akalonga a Yuda pamodzi ndi chigulu chawo chimene chikuchita phokoso,Palinso akalonga a Zebuloni komanso akalonga a Nafitali. 28  Mulungu wanu waganiza kuti akupatseni mphamvu. Sonyezani mphamvu zanu, Inu Mulungu, amene mumatithandiza.+ 29  Chifukwa cha kachisi wanu yemwe ali ku Yerusalemu,+Mafumu adzabweretsa mphatso kwa inu.+ 30  Dzudzulani nyama zakutchire zimene zimakhala mʼmabango,Gulu la ngʼombe zamphongo+ limodzi ndi ana awo,Mpaka mitundu ya anthu itagwada nʼkubweretsa ndalama zasiliva. Koma iye wabalalitsa mitundu ya anthu imene imasangalala ndi nkhondo. 31  Zinthu zopangidwa ndi kopa* zidzabwera kuchokera* ku Iguputo,+Mwamsanga, dziko la Kusi lidzapereka mphatso kwa Mulungu. 32  Inu maufumu a dziko lapansi, imbirani Mulungu,+Imbani nyimbo zotamanda Yehova, (Selah) 33  Imbirani iye amene wakwera pamwamba pa kumwamba,+ kumene kwakhalapo kuyambira kalekale. Mawu ake amphamvu amamveka ngati bingu. 34  Vomerezani kuti Mulungu ndi wamphamvu zochuluka.+ Ulemerero wake uli pa Isiraeli,Ndipo amasonyeza mphamvu zake kuchokera kumwamba.* 35  Mulungu walamula kuti anthu amuope komanso amupatse ulemu mʼmalo ake opatulika aulemerero.+ Iye ndi Mulungu wa Isiraeli,Amene amapereka mphamvu ndi nyonga kwa anthu.+ Mulungu atamandike.

Mawu a M'munsi

^ Mabaibulo ena amati, “akudutsa mʼmitambo.”
^ “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amaweruzira milandu.”
^ Kapena kuti, “opanduka.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “cholowa chanu chimene chinali chofooka.”
^ Limeneli ndi lamulo loti apite kunkhondo.
^ Umenewu ndi uthenga wonena za kupambana pankhondo.
^ Kapena kuti, “ndi zagilini wopitira kuyelo.”
^ Mabaibulo ena amati, “Zinali ngati matalala akugwa pa Zalimoni.” Kapena kuti, “chipale chofewa.”
^ Kapena kuti, “phiri laulemerero.”
^ Kapena kuti, “wafuna.”
^ “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
^ Kapena kuti, “amene akuyenda mʼnjira yochimwa.”
^ Kapena kuti, “mkuwa.”
^ Mabaibulo ena amati, “Nthumwi zidzachokera ku.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmitambo.”