Salimo 18:1-50
Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la mtumiki wa Yehova, Davide, amene anauza Yehova mawu amʼnyimbo iyi pa tsiku limene Yehova anamulanditsa mʼmanja mwa adani ake onse komanso mʼmanja mwa Sauli. Iye anati:+
18 Ndimakukondani inu Yehova, mphamvu yanga.+
2 Yehova ndi thanthwe langa, malo anga achitetezo ndiponso amene amandipulumutsa.+
Mulungu wanga ndi thanthwe langa+ limene ndimathawirako,Iye ndi chishango changa, nyanga* yanga ya chipulumutso* komanso malo anga othawirako otetezeka.*+
3 Ndidzaitana Yehova, amene ndi woyenera kutamandidwa,Ndipo adzandipulumutsa kwa adani anga.+
4 Zingwe za imfa zinandikulunga,+Gulu la anthu opanda pake, amene anali ngati madzi osefukira, ankandiopseza.+
5 Zingwe za Manda* zinandizungulira.Ananditchera misampha ya imfa.+
6 Pa nthawi ya mavuto anga ndinaitana Yehova,Ndinapitiriza kufuulira Mulungu wanga kuti andithandize.
Iye anamva mawu anga ali mʼkachisi wake,+Ndipo makutu ake anamva kulira kwanga kopempha thandizo.+
7 Kenako dziko lapansi linayamba kugwedezeka ndi kunjenjemera.+Maziko a mapiri ananjenjemera,Komanso anagwedezeka chifukwa Mulungu anakwiya.+
8 Utsi unatuluka mʼmphuno mwake,Ndipo moto wowononga unatuluka mʼkamwa mwake.+Makala oyaka anatuluka mwa iye.
9 Iye anaweramitsa kumwamba pamene ankatsika,+Ndipo mdima wandiweyani unali pansi pa mapazi ake.+
10 Iye anakwera pakerubi ndipo anabwera akuuluka.+
Mulungu anauluka mwaliwiro pamapiko a mngelo.*+
11 Kenako anadziphimba ndi mdima,+Panali madzi akuda ndi mtambo wakuda+Zimene zinamuzungulira ngati tenti yake.
12 Kuwala kunangʼanima pamaso pake,Ndipo matalala ndi makala a moto anatuluka mʼmitambo.
13 Kenako Yehova anayamba kugunda ngati mabingu ali kumwamba.+Wamʼmwambamwamba anachititsa kuti mawu ake amveke,+Ndipo kunagwa matalala ndi makala a moto.
14 Anaponya mivi yake nʼkuwabalalitsa.+Anaponya mphezi zake nʼkuwachititsa kuti asokonezeke.+
15 Pansi pa mitsinje* panayamba kuonekera.+Maziko a dziko lapansi anayamba kuonekera chifukwa cha kudzudzula kwanu, inu Yehova,Komanso chifukwa cha mphamvu ya mpweya wotuluka mʼmphuno mwanu.+
16 Anatambasula dzanja lake kuchokera kumwamba,Anandigwira nʼkundivuula mʼmadzi akuya.+
17 Anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu,+Kwa anthu odana nane amene anali amphamvu kuposa ine.+
18 Adaniwo anandiukira pa tsiku la tsoka langa,+Koma Yehova anandithandiza.
19 Ananditenga nʼkundiika pamalo otetezeka.*Anandipulumutsa chifukwa ankasangalala nane.+
20 Yehova amandidalitsa mogwirizana ndi chilungamo changa.+Amandipatsa mphoto chifukwa choti ndine wosalakwa.*+
21 Ndasunga njira za Yehova,Ndipo sindinachite chinthu choipa kwambiri, chomwe ndi kusiya Mulungu wanga.
22 Ndimakumbukira ziweruzo zake zonse,Ndipo sindidzanyalanyaza malamulo ake.
23 Ndidzakhalabe wosalakwa pamaso pake,+Ndipo ndidzayesetsa kupewa cholakwa.+
24 Yehova andipatse mphoto chifukwa choti ndine wolungama,+Komanso chifukwa choti ndine wosalakwa pamaso pake.+
25 Munthu wokhulupirika, mumamuchitira zinthu mokhulupirika.+Munthu wopanda cholakwa, mumamuchitira zinthu mwachilungamo.+
26 Kwa munthu woyera, mumasonyeza kuti ndinu woyera,+Koma kwa munthu wopotoka maganizo mumasonyeza kuti ndinu wochenjera.+
27 Inu mumapulumutsa anthu onyozeka,*+Koma anthu odzikweza* mumawatsitsa.+
28 Chifukwa inuyo Yehova ndi amene mumayatsa nyale yanga,Mulungu wanga amandiunikira mumdima.+
29 Ndi thandizo lanu, ndingalimbane ndi gulu la achifwamba.+Ndi mphamvu za Mulungu ndingakwere khoma.+
30 Njira ya Mulungu woona ndi yangwiro.+Mawu a Yehova ndi oyengeka bwino.+
Iye ndi chishango kwa anthu onse amene amathawira kwa iye.+
31 Kodi pali Mulungu winanso woposa Yehova?+
Nanga pali thanthwe linanso kupatula Mulungu wathu?+
32 Mulungu woona ndi amene amandipatsa mphamvu,+Ndipo adzasalaza njira yanga.+
33 Iye amachititsa mapazi anga kuti akhale ngati a mbawala,Amachititsa kuti ndiime pamalo okwera.+
34 Iye amaphunzitsa manja anga kumenya nkhondo,Manja anga angathe kukunga uta wakopa.*
35 Inu mumandipatsa chishango chanu chachipulumutso,+Dzanja lanu lamanja limandithandiza,*Ndipo kudzichepetsa kwanu nʼkumene kumandikweza.+
36 Mumakulitsa njira kuti mapazi anga azidutsamo,Ndipo mapazi anga sadzaterereka.+
37 Ndidzathamangitsa adani anga nʼkuwapeza,Sindidzabwerera mpaka onse nditawawononga.
38 Ndidzawaphwanya kuti asadzukenso.+Ndidzawapondaponda ndi mapazi anga.
39 Inu mudzandipatsa mphamvu kuti ndithe kumenya nkhondo.Mudzachititsa kuti adani anga agonje.+
40 Mudzachititsa kuti adani anga athawe pamaso panga,*Ndipo ndidzapha* anthu amene amadana nane.+
41 Iwo amafuula kuti athandizidwe, koma palibe amene angawapulumutse,Amafika pofuulira Yehova, koma iye samawayankha.
42 Ndidzawapera ndipo adzakhala ngati fumbi louluzika ndi mphepo.Ndidzawakhuthula ngati matope mumsewu.
43 Inu mudzandipulumutsa kwa anthu a mtundu wanga ondipezera zifukwa.+
Mudzandiika kuti ndikhale mtsogoleri wa mitundu ya anthu.+
Anthu amene sindikuwadziwa adzanditumikira.+
44 Anthu akadzangomva mphekesera zokhudza ine, adzandimvera.Anthu ochokera mʼdziko lina adzandigwadira mwamantha.+
45 Anthu ochokera mʼdziko lina adzachita mantha,*Iwo adzatuluka mʼmalo awo otetezeka akunjenjemera.
46 Yehova ndi wamoyo. Litamandike Thanthwe langa.+
Mulungu amene amandipulumutsa alemekezeke.+
47 Mulungu woona amabwezera adani anga.+Iye amachititsa kuti mitundu ya anthu izindigonjera.
48 Iye amandipulumutsa kwa adani anga olusa.Mumandikweza pamwamba pa anthu amene amandiukira.+Mumandipulumutsa kwa munthu wachiwawa.
49 Nʼchifukwa chake ndidzakulemekezani, inu Yehova, pakati pa mitundu ya anthu.+Ndipo ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.+
50 Iye amachita zazikulu kuti apulumutse mfumu yake,+Amasonyeza chikondi chokhulupirika kwa wodzozedwa wake,+Kwa Davide ndi mbadwa* zake mpaka kalekale.+
Mawu a M'munsi
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “mpulumutsi wanga wamphamvu.”
^ Kapena kuti, “malo okwezeka achitetezo.”
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “pamapiko a mphepo.”
^ Kapena kuti, “ngalande zamadzi.”
^ Kapena kuti, “otakasuka.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “chifukwa choti manja anga ndi oyera.”
^ Kapena kuti, “ovutika.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “a maso odzikweza.”
^ Kapena kuti, “wamkuwa.”
^ Kapena kuti, “limandichirikiza.”
^ Kapena kuti, “Mudzandipatsa msana wa adani anga.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ndidzakhalitsa chete.”
^ Kapena kuti, “mphamvu zidzawathera.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”